Nkhani

Boma likukhazikitsa misika ya zakudimba

Listen to this article

Boma lili mkati momanga malo ogulitsira zokolola zakudimba ngati njira imodzi yochulukitsira phindu lomwe alimi amapeza pogulitsa zokolola zochokera mu ulimi wamthirira.

Ntchitoyi ndi gawo limodzi la ntchito yotukula ulimi wamthirira pokonzanso masikimu 11 m’chigawo cha zaulimi cha Blantyre Agricultural Development Division (ADD).Farmers in a cabbage field

Mkulu woyang’anira ntchito yotukula zipangizo za ulimi wamthirira, Cosmos Luwanda wati misikayi, yomwe ilipo 6, imangidwa ku Neno ndi kuchigwa cha mtsinje wa Shire.

Iye wati ntchitoyi, yomwe ikugwirika ndi thandizo la ndalama zokwana 12 biliyoni kwacha kuchokera ku African Development Bank (ADB), imanga manthu wa misika mumzinda wa Lilongwe komwe kutakhale zipangizo zapamwamba zotha kusungira ndiwo zamasamba ndi zipatso kwanthawi yaitali.

“Cholinga cha misikayi ndi kulumikiza alimi ndi ogula mosavuta,” adatero Luwanda.

Mkulu woyang’anira ntchito yomanga msika wa zokolola za kudimba wa Chikwawa, Khama Kammwamba, adati malowa adzakhala ndi malo osungira zokolola, malo otsukira zokolola, magetsi, madzi apampopi ndi zimbudzi zamakono.

“Misikayi izidzagulitsa zokolola mwachipiku kwa amalonda ochokera kutali. Adindo oyendetsa masikimu ndi amene azidzayendetsa misika imeneyi,” adatero Kammwamba.

Padakalipano ntchito yokonza masikimu amene ali mupolojeikiti imeneyi ili mkati ndipo masikimuwa akuyembekezeka kuyamba kugwira ntchito yawo usanafike mwezi wa June chaka chamawa.

Mabanja 12 000 ndiwo akuyembekezeka kupindula ndi ntchito zosiyanasiyana zomwe zitatumphuke muchitukuko cha ulimi wamthirira ndi misika ya zokolola za kudimbayi. Mabanja 4 000 akuyembekezeka kuswa mphanje ya ndime ya mthirira yokwana mahekitala 1 601.n

Related Articles

Back to top button