Nkhani

‘Boma likutengera a Malawi kumtoso’

Listen to this article

Pamene nkhani ya malamulo oyendetsera zisankho ili mkamwamkamwa, mkulu womenyera ufulu wa anthu, John Kapito, wati nkhani za magetsi, madzi ndi kulowa pansi kwa chuma ndi zofunika kuti ziunikidwe mozama ndi Nyumba ya Malamulo yomwe yayamba dzuloyi.

Kapito amathirirapo ndemanga pankhani yomwe yamanga nthenje yoti aphungu a nyumbayo sakambirana malamulo azisankho kaamba koti nduna sizidathe kuwaunika.

Kayendetsedwe ka chisankho sikasintha aphungu akapanda kukambirana malamulo atsopano

Izi zakwiyitsa mabungwe omenyera ufulu wa anthu a Centre for the Development of People (Cedep) ndi Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR) omwe adapempha aphungu kuti anyanyale nkhumano wa nyumbayo mpaka boma litaika pamndandanda wa zokambirana malamulo atsopano oyendetsera zisankho.

Koma Kapito akuti ngakhale nkhaniyo ili yofunikira kwambiri, mavuto a magetsi, madzi ndi kulowa pansi kwa chuma ndi zinthu zofunika kuthana nazo mwachangu.

“Anthu ambiri akupanga phokoso kwambiri ndi malamulo oyendetsera zitsankho. N’zoona malamulowo ndi ofunika, koma pali nkhani zina zofunika kwambiri zomwe anthu sakuzitchula. Tiyeni tiunike vuto la magetsi, madzi ndi chuma omwe akhudza miyoyo ya Amalawi ambiri,” adatero Kapito.

Iye adati kulimbikira kuti nyumbayo ikambirane malamulo azisankho n’kusiya mavutowa n’chimodzimodzi bambo kumasunga ndalama zogulira galimoto pamene ana ake akusowa chakudya, zovala, komanso athamangitsidwa fizi ku sukulu.

Padakali pano komiti yoona zokambirana za nyumbayo yatsimikiza kuti pali malamulo 6 omwe aphungu akambirane, koma Kapito wati sakuonapo lamulo lomwe lingathandize Amalawi mwachangu potengera ndi mavuto omwe akukumana nawo.

“Ndaunika malamulo onse omwe ali pamndandanda woti nyumbayo ikambirane, koma palibe lamulo lomwe lithane ndi vuto la magetsi, madzi, komanso kukweza chuma cha dziko lino.

Koma Billy Mayaya, yemwe ndi wodziwika kwambiri pankhani yomenyera ufulu wa anthu, wati boma likutengera Amalawi kumtoso posaika malamulo a zisankho pamndandanda wa zokambirana.

“N’zomvetsa chisoni kuti andale amafuna anthu panthawi yovota, koma kuti apange zofuna zawo amayang’ana kumbali,” adatero mkuluyu.

Mayaya adati malamulo a zisankho ndi ndime yoyamba yoonesetsa kuti Amalawi akulamulidwa ndi anthu omwe akuwafuna.

Imodzi mwa nkhani zikuluzikulu zomwe zili mu lamulolo n’kuonetsetsa kuti boma lililonse mukhale dera lomwe amayi okhaokha azipikitsana pampando wa phungu.

Anthu ena omwe akhala akumenyera ufulu wa amayi akuti boma likulakwa kaamba kosatengera malamulowo ku Nyumba ya Malamulo.

Mmodzi mwa amayi omwe amamenyera ufulu wa amayi, Emmie Chanika, adati vuto la Amalawi n’kuyang’anira vuto mpaka likule ngati momwe mwana amayang’anira chilonda mpaka chikule n’kufika potukusira.

“Amalawi, zitsanzo tili nazo za maiko omwe adapatsa amayi mpata ndipo lero akuchita bwino. Nanga ife tidzapereka liti mpata kwa amayi?” adafunsa Chanika.

Iye adati anthu ambiri sachitapo kanthu pankhani zaphindu monga zotukula miyoyo ya amayi, koma nkhani zopanda pake.

Mabungwe a Cedep ndi CHRR adapempha aphungu kuti anyanyale nkhumano ya Nyumba ya Malamulo mpaka boma litabweretsa nyumbayo malamulo a zisankho.

Mkulu wa Cedep, Gift Trapence, ndi wa CHRR, Timothy Mtambo, adapempha boma kuti lichite zofuna za anthu potengera malamulowo ku nyumbayo.

Bungwe la Public Affairs Committee (PAC), lomwe posachedwapa limachititsa misonkhano yokambirana za malamulowo, lati silidayembekezere kuti boma lingawadyetse njomba yotere.

Mwa zina, malamulowo akuti mtsogoleri yemwe wachita bwino pa zisankho azilumbilitsidwa pakatha masiku 30 kuchokera patsiku loulutsa zitsakho, komanso kuti azipeza mavoto oposa theka la anthu omwe adaponya mavotiwo. Malamulowo akufunanso kuti m’boma lililonse mukhale dera lomwe amayi okhaokha azipikitsana pampando wa phungu.

Malamulowo akufuna kuti bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lizipatsidwa ndalama zokwanira kuti ntchito zake ziziyenda bwino.

Related Articles

Back to top button