Nkhani

Boma lilonga mafumu 250

Boma kudzera muunduna wa za maboma aang’ono latsimikiza kuti mafumu 250 aikidwa pamndandanda wolandira nawo mswahara kupangitsa kuti ndalama zopita ku thumba la mafumuwa zikwere.

Nduna ya maboma aang’ono, Kondwani Nankhumwa, wati nkhani ya mafumu ili choncho chifukwa ntchitoyi idayambika kale ndi mtsogoleri wakale Joyce Banda ndipo boma la DPP likungopitiriza ndondomekoyi.Mafumu_closeup

“Mafumuwa adawakweza ndi mtsogoleri wakale Joyce Banda koma adali asadawaike pamndandanda wolandira ndalama komanso ena adali asadalamulidwe kuti ayambe kugwira ntchito yawo.

“Chomwe boma la DPP lapanga, ndi kuwalonga mafumuwa kuti ayambe kugwira ntchito komanso kuwaika pamndandanda woti ayambe kulandira mswahara,” adatero Nankhumwa, pocheza ndi Tamvani pafoni.

Nankhumwa wati boma la DPP lakweza mafumu awiri okha omwe ndi Ngolongoliwa ndi Toleza koma ena onse adakwezedwa ndi Banda.

Ma Paramount amalandira K50 000, Senior Chief K30 000, T/A K18 000, Sub T/A K8 000, magulupu K5 000 ndi nyakwawa K2 500.

Nankhumwa akuti pakadali pano K1.7 biliyoni ndiyo ikugwiritsidwa ntchito kulipirira mswahara wa mafumuwa ndipo wati ndi kuonjezereka kwa enaku kupangitsa kuti ndalamazi zifike pafupifupi K2.5 biliyoni.

Izi zikudza pamene maunduna ena ofunika monga a zamaphunziro ndi zaumoyo alandidwa ndalama zina kupangitsa kuti maundunawa alephere kulemba aphunzitsi ndi anamwino ena.

Yemwe amathirira ndemanga pa nkhani zaumoyo ndi zipatala, Martha Kwataine, komanso kadaulo pa ndale Henry Chingaipe adzudzula izi ndipo ati kulibwino ndalamazi zipite maunduna.

Dziko lino lili pampanipani wa zachuma, zomwe zachititsa kuti boma lichepetse ndondomeko ya zachuma ndi K23 biliyoni chifukwa chomanidwa thandizo ndi maiko amene akhala akulithandiza.

Nankhumwa adavomereza akuti ndalama zomwe ziyambe kupita kwa mafumuwo ndi zambiri ndipo zidakathandizadi maunduna ena amene ali pampanipani monga unduna wa zaumoyo komanso wa zamaphunziro.

“Timanenedwa ndipo mafumuwo amati mwina sitikuwapatsa malipiro chifukwa adakwezedwa ndi boma la People’s Party (PP). Ndiye taona kuti nkofunika kuti tiwaike pamndandanda woti azilandira mswahara kuyambira tsopano,” adaonjeza Nankhumwa.

“Apapa zidalakwika kale ndiye sitingachitire mwina. Inde tilibe ndalama, koma nanga tikadatani? Chifukwa izi zikadapereka mavuto ena achikhala kuti tidawasiya kuti mafumuwo asamalandire [mswahara].”

Mafumu ena ayamba kale mwezi wathawu kulandira mswahara wawo malinga ndi ganizo la boma lowaika pamndandandawu. Mafumu 20 akwezedwa kale mwezi wa February m’chigawo cha kummwera.

Koma Kwataine akuti boma lidziwe kuti kulakwitsa kuwiri sikungabweretse mayankho kwa anthu, ndipo yati boma likadaganiza kawiri.

“Anthu akusowa mankhwala ndi zakudya m’zipatala ndiye boma likuchotsa ndalama ku unduna wa zaumoyo kukapatsa mafumu? Boma litaunikapo bwino pamenepa,” adatero Kwataine.

Iye adati sikulakwitsa kusiya kaye kukweza mafumu bola nthambi zina zinthu zikuyenda bwino malinga ndi mavuto a zachuma omwe dziko lino likukumana nawo pakalipano.

“Anthu akulipa nkhuku ndi mbuzi kubwalo la mfumu, kodi zimenezi si zokwanira kwa mafumuwa? Ngakhale kuwasiya osamawapatsa ndalama palibe vuto chifukwa malipiro awo amapezeka kumudzi komweko.

“Panopa m’midzi anthu akungophana pena kumenya anthu okalamba kusonyeza kuti anthu adataya chikhulupiriro mwa mafumu. Ndiye palinso chifukwa chowapatsira ndalama zambiri ngati zimenezi?” adafunsa Kwataine.

Naye Chingaipe wati kulakwika kudachitika ndi boma la PP komabe boma la DPP likadaona nthawi yochitira izi.

“Si zobisa, dziko lino lili pamavuto a zachuma, ndiye nchifukwa chiyani boma laganiza kuti achite izi lero pamene zinthu sizilibwino?

“Panopa mafumu akukhudzidwa ndi ndale, nchifukwa chake ndikufuna kuti bwanji boma laganiza zowaika pa mndandanda wolandira ndalama mafuwa lero?” adatero Chingaipe.

Mneneri mu undunawu, Muhlabase Mughogho wati ntchitoyi sidayambe lero ndipo ili mkati mpaka mafumu otsalawa atathananawo.

“Sitinganene kuti mafumu otsalawo tithananawo liti koma ntchito ili mkati,” adatero mneneriyu.

Iye adati mafumu 41 900 ndi amene akhala akulandira mswahara mwa mafumu 42 150 amene ali m’dziko muno, kusonyeza kuti mafumu 250 ndi amene sadayambe kulandira.

Mafumu amene akwezedwa mwezi wa February ndi T/A Nchiramwera wa ku Thyolo; Senior Chief Ngolongoliwa ya m’boma la Thyolo; Senior Chief Kuntaja wa m’boma la Blantyre; Senior Chief Kanduku ya m’boma la Mwanza; T/A Ngowe ya m’boma la Chikwawa komwe ufumuwu waima kaye pamene nkhani yapita kubwalo.

Ena amene akwezedwa ndi T/A Ndamera ya m’boma la Nsanje; Sub T/A Toleza ya m’boma la Balaka; Sub T/A Phalula ya m’boma la Balaka; ku Machinga kuli Sub T/A Sale, T/A Nkoola, T/A Nkula, kudzanso Sub T/A Lulanga ndi Mtonda a m’boma la Mangochi.

Chigawo chapakati ndi kumpoto kwakwezedwanso mafumu 11 ndipo ena akwezedwa miyezi ikudzayi.

Related Articles

Back to top button