Nkhani

Boma lipereka katemera winanso wa polio

Listen to this article

Womenyera ufulu pa nkhani zaumoyo, a George Jobe akumema makolo ndi onse omwe akusunga ana kuti aonetsetse kuti ana awo alandira katemera woonjezera wa polio yemwe boma liyambe kupereka pa 21 mwezi uno.

Katemera woonjezerayu aperekedwa kwa ana pafupifupi 2.9 miliyoni osachepera zaka 5 m’dziko lino ngati njira imodzi yochepetsera kufala kwa matendawa. Polio adapezeka kotsiriza m’chaka cha 2005 m’Malawi lino.

Izi zikuchitika potsatira kupezeka kwa polio pa mwana wa zaka zitatu ku Lilongwe mu mwezi wa February, zomwe zachititsa kuti boma lilamule kuti ana onse a misinkhu imeneyi, ngakhale omwe adalandira kale katemerayu alandirenso katemera wa polio akayambiranso kulandiritsa.

Ana omwe ali pachiopsezo kwambiri ndi omwe sadalandirepo katemera wa polio komanso omwe adalumphitsapo katemerayu.

A Jobe adati china chimene chikufunika ndi kuuza anthu ngati boma ndi mabungwe za kufunikira koti mwana akalandire katemerayu ndi cholinga choti anawo atetezedwe ku polio, zomwe ndi zotheka kudzera m’katemerayu.

Katemera wa polio-yu amapezeka ku sikelo komwe makolo amapititsa ana awo, ndipo a Jobe adati ana omwe sadalandire katemerayu ndi chifukwa cha kunyalanyaza kwa makolo awo.

“Boma lalengeza kuti pakhala katemera wina wa polio chifukwa choti mwana wina wapezeka ndi polio ku Malawi kuno, ndipo pozindikira kuti pali makolo ena omwe akhala akulumphalumpha kupititsa ana awo ku katemera wa polio, ndi chifukwa chake pabwera kulengeza kumeneku.

“Katemerayu alipo wambiri. M’zipatala zathu katemera wa polio amaperekedwa kanayi. Mwana akangobadwa kumene amalandira polio zero, kenaka polio 1 mpaka 3. Palinso katemera wa chifuwa chachikulu, wa penta, wa chikuku ndi ena,” adatero a Jobe.

Katemera wa polio wakhala akuperekedwa m’dziko lino, ndipo akatswiri pnkhani za umoyo adati Malawi ikuchita bwino ndithu ku mbali yolandira katemera wa polio yu.

Mkulu woona nkhani za katemera mu unduna wa zaumoyo, Dr Mike Chisema ali ndi chikhulupiliro kuti matenda a polio sapitirira kufala potengera kuti ana oposa makumi 8 mwa 100 ali onse m’dziko lino adalandira katemera wa polio kudzera m’ntchito zopereka katemera zomwe undunawu ukugwira.

Iwo adakambanso kuti mwa ana 200 ali wonse ogwidwa ndi polio, mmodzi amalumala nayo ndipo pakati pa ana 5 ndi 10 mwa 100 ali onse ogwidwa ndi nthendayi amatha kutaya miyoyo yawo chifukwa cha kusagwira ntchito bwino kwa njira zopumira.

Posachedwapa, wachiwiri kwa nduna ya za umoyo, a Enock Phale adati boma lichita izi mogwirizana ndi othandiza boma osiyanasiyana. Padakalipano ali pa kalikiliki kudziwitsa mtundu wa Malawi za kubwera kwa katemera owonjezerayu.

Related Articles

Back to top button
Translate »