Nkhani

Boma lipereka mavidiyo a JB, Lutepo ku ACB

Listen to this article

Boma Lachinayi lidati lapereka kubungwe lothana ndi ziphuphu la Anti-corruption Bureau (ACB) mavidiyo a mtsogoleri wakale wadziko lino Joyce Banda akukambirana ndi Oswald Lutepo yeme akumuganizira kuti ndiye adasolola ndalama za kashigeti zochulukitsitsa.

Koma bungwe la ACB Lachinayi lomwelo lidati silidalandire mavidiyowo ndipo ofesi ya Banda idati siyidaone chikalata cha bomacho kuti ayankhepo kanthu.

Chikalatacho chimene chidali patsamba la boma la pa Internet chidati mafilimuwo alipo 23 ndipo awiriwo ankakumana kunyumba za boma za Sanjika, Chikoko Bay, Kamuzu Palace ndi Mzuzu State Lodge.

Chikalatacho chidati: “Nthawi zina awiriwo amakumana okhaokha ndipo pena pamakhala anthu ena angapo kuphatikizapo atsogoleri a chipani cha PP.”

Koma wachiwiri kwa mkulu wa ACB Reyneck Matemba adati bungwelo silidalandire mafilimuwo ndipo sakudziwa kalikonse pankhaniyo.

“Ndafunsa bwana wanga [mkulu wa ACB] ngakhalenso ofufuza amene akutsata nkhaniyi koma onse akuti sakudziwapo kanthu,” adatero Matemba.

Ndipo mthandizi wa Banda, Andekuche Chanthunya adati sadachione chikalatacho ndipo sangayankhepo kanthu.

Lutepo adali mmodzi mwa a chipani cha PP pomwe chinali m’boma. Boma latulutsa chikalatacho patatha sabata ziwiri kuhokera pomwe Lutepo adauza wailesi ya Zodiak kuti aulula Banda za momwe awiriwo amagwirizanirana kupakula ndalama zaboma.

Koma mkulu wa oimira boma pamilandu Mary Kachale adati Lutepo amayenera kukanenera izo kukhoti.

Related Articles

Back to top button