Nkhani

Boma litemera ziweto 10 000

Listen to this article

Pofuna kuthana ndi mliri wa matenda a zilonda za m’ mapazi ndi m’mkamwa a ng’ombe omwe agwa m’boma la Chikwawa, boma lakonza zopereka katemera ku ziweto zoposa 10 000 m’chigwa cha Shire posachedwapa.

Mlembi wa unduna wa zamalimidwe, ulimi wamthirira ndi chitukuko cha madzi, Erica Maganga, watsimikizira Uchikumbe kuti boma laitanitsa kale mankhwala a katemerayu kuchoka kudziko la Botswana.cow

“Pakalipano mankhwala ali m’njira ndipo akhala akufika tsiku lina lililonse kuti ntchito yopereka katemera iyambike,” adatero Maganga Lolemba.

Iye adati boma lachita machawi poitanitsa katemerayu pofuna kuti matendawa asafalikire m’madera ena komanso pofuna kuteteza ntchito zina za ulimi monga ulimi wa mkaka.

Boma lidakhazikitsa chiletso cha malonda a nyama ndi kutulutsa kapena kulowetsa ziweto m’boma la Chikwawa zitatsimikizika kuti m’bomali mudagwa mliri wa matendawa omwe pachizungu amati Foot and Mouth Disease.

Unduna wa zamalimidwe, ulimi wamthirira ndi chitukuko cha madzi udatsimikiza za mliriwu womwe akuti udasautsa pamalo ena osambitsirapo n’gombe a Mthumba omwe ali m’gawo loyang’anira za ulimi la Mitole EPA.

M’chikalata chomwe Maganga adasayinira sabata yatha, undunawu udati chigodola cha ng’ombe ndi nthenda yovuta kwambiri ndipo imagwira ziweto monga ng’ombe, mbuzi, nkhosa ndi nkhumba komanso nyama zakutchire monga njati.

Potsirapo ndemanga pamliriwu, wachiwiri kwa mkulu woyendetsa ntchito za zaumoyo wa ziweto ndi ulimi wa ziweto, Dr Patrick Chikungwa, adati nthendayi ndi yowopsa kwambiri ndipo ngati yalekereredwa imafala msanga.

Nthendayi imafala kudzera mumpweya, kukhudzana kapena kudya msipu womwe uli ndi tizilombo (virus) toyambitsa matendawa, adatero Chikungwa. Adaonjezera kunena kuti anthunso atha kufalitsa tizilombo ta nthendayi kudzera m’zovala kapena nsapato, koma adati alimi asade nkhawa chifukwa boma likuchita zothekera kuti nthendayi isafalikire madera ena.

Iye adati zizindikiro za nthendayi ndi kuchucha malovu, matuza mkamwa komanso pakati pa zikanamba za miyendo zomwe zimapangitsa kuti ng’ombe izivutika poyenda.

“Ngati mlimi aona zizindikirozi, chomwe ayenerea kuchita n’kupatula ziweto zodwalazi kuti zisakhudzane ndi zimene sizinakhudziwe ndi nthendayi,” Chikungwa adalangiza.

Mkuluyu adati zilondazi zikaphulika zitha kupola pogwiritsa ntchito mankhwala monga ma antibayotiki a ziweto. n

Related Articles

Back to top button