Chichewa

Boma lititeteze, atero achitetezo

Listen to this article

 

Anthu okhwimitsa chitetezo m’mudzi mwa Ntenje, m’dera la T/A Machinjiri m’boma la Blantyre, apempha boma kuti liwateteze ndi kuwasamala pamene akusaka malo obisala.

Iwo ati pantchito yawo monga odzipereka, samalandira kalikonse koma pofuna kuteteza mudzi wawo, kwapezeka kuti nyumba zawo zatenthedwa, katundu waonongedwa. Miyoyo yawo ili pachiswe; iwo ndi mabanja awo akusowa pokhala; ndipo akubisala m’tchire.

Police_chimbaula

Kumayambiriro a mwezi uno anthu okwiya a m’mudziwo adabutsa nyumba zawo, kuwakumbitsa manda komanso kuwamenya powaganizira kuti adapha munthu.

Monga akufotokozera mmodzi mwa achitetezowo, Davie Story, iwo ankateteza Nyadani Dankeni kuti asachitidwe chipongwe ndi anthu okwiyawo amene ankamumenya chifukwa chomuganizira kuti adaba thumba la chimanga.

Iye adati anthuwo adayatsa nyumba zawo ndipo palibe chomwe adapulumutsapo. Adawakumbitsa manda komanso kuwatibula kodetsa nkhawa. Achitetezo onsewo athawamo m’mudzimo ndipo akubisala m’tchire.

Mkulu wa achitetezowo, Damiano Dindi, adati iye adawathawira ku Nsanje.

“Palibe chomwe ndapulumutsa. Chonde, tikupempha boma kuti litithandize chifukwa tazingwa, tilibe pogwira komanso kolowera. Atipezere pokhala komanso atipatse mpamba woti tiyambire moyo wina,” adatero Dindi.

Related Articles

Back to top button
Translate »