Chichewa

Boston Kabango: Chikhomo cha Wanderers

Listen to this article

 

Kungomva za Boston Kabango, omwetsa zigoli a matimu ena amayamba kunjenjemera kaamba ka ntchito za mnyamatayu zomwe amazionetsa ku Mighty Be Forward Wanderers komanso ku Flames Under 20. Kodi ntchito zake n’zotani? Adayamba bwanji? Nanga tsogolo akuliona bwanji? BOBBY KABANGO akucheza naye motere:

Mpira si dzitho: Kabango
Mpira si dzitho: Kabango

Kodi Boston amamveka uja ndiweyo?

Ndine ndithu, musaderere ndi maso okha koma muzipita pabwalo kuona luso lomwe Mulungu adapereka. Dzina langa lonse ndi Boston ‘Bosnho’ Kabango.

Thupi limeneli umatha kulimbana ndi osewera amatupi awo?

Nchifukwa ndikuti musaderere, mpira si kukula thupi koma kukhala ndi mphamvu za mpirawo. Ine ndimayesetsa kuti ndizichita mafizo kuti ndikhale ndi mphamvu zosewerera mpira, osati zoti anthu azindiona nazo.

Kodi udayamba liti kusewera mpira?

Luso lidaoneka ndikusewera ku Sporting Leopards mu 2010. Titapita kukapikisana nawo kumpikisano wa Zone 6 anthu adagoma ndi luso langa ndipo Azam Tigers idanditenga. Mu 2015 mpamene ndimabwera ku Nyerere.

Moyo ku Nyerere uli bwanji?

Zonse zili bwino, pena tikhumudwe pena kusangalala ndimo moyo umayendera. Kungoti pakati ndidali wovulala ndiye ndatenga nthawi osasewera, pano ndabwereramo.

Uli ndi zaka zingati? Pajatu mumabera zaka anyamata a mpira inu…

Hahaha! Ayinso osati kubera koma ndili ndi zaka 20.

Maphunziro ndi otani? Nanga uchitanso ziti kupatula mpira?

Ndadutsa fomu 4 moti ndikufuna ndipange za umekaniki koma posakhalitsapa ndipitanso kusukulu. Ndimafunitsitsa ntchitoyi kupatula kuti Mulungu adandidalitsa ndi luso la mpira.

Umalota utadzafikira pati?

Kukasewera ku England, ilili ndiye loto ndikamasewera mpira.

Ndani amakudolola? Nanga ukafatsa umakonda chiyani?

Limbikani Mzava komanso kunja ndi Gary Cahill. Ngati sindikusewera mpira ndiye ndimakonda kuonera makatuni komanso kucheza ndi mayi anga.

Kodi ku Nyerere kuli tsogolo?

Ndi timu yaikulu, inunso mukudziwa zimenezo. Ukamasewera matimu ngati Wanderers kapena Bullets utachita zakupsa utha kukafuka patali ndi mpira wako. n

Related Articles

Back to top button