Nkhani

Bullets iphana ndi Wanderers lero

Listen to this article

Ambiri adakamba kuti mwina masewero a lero pakati pa Bullets ndi Wanderers mu TNM Super League alephereka ponena kuti osewera akukatumikira Flames, koma izo ndi nkhani yakale chifukwa lero ntchito ilipo pa Kamuzu Stadium.

Kochi wa Flames Ernest Mtawali Lachinayi adawalola osewera kuti akatumikire matimu awo. Osewerawo adangololedwa kuti asewere masewero alero ndipo abwerere ku Flames madzulo alero.bullets

Bullets idachinya Wanderers m’ndime yoyamba 2-1 ndipo Wanderers idabweza chipongwe mu Carlsberg Cup pamene idapambana 2-1.

Lero kamuna ndani? Mphunzitsi wa Wanderers Elijah Kananji akuti timu yake yakonzeka ngakhale palibe osewera monga Jabulani Linje ndi Rafiq Mussa chifukwa chovulala.

Pamene Mabvuto Lungu wa Bullets akuti nawonso akonzeka komabe timu yawo isowa ntchito za Chiukepo Msowoya, Owen Chaima ndi Vincent Gona chifukwa chovulala pamene Sankhani Mkandawire wabwerera.

Related Articles

Back to top button