Nkhani

Bullets yayamba ndi ukali

Listen to this article

Timu ya Big Bullets, yomwe ikuteteza chikho cha TNM Super League, yayambanso ndi ukali m’ndime yachiwiri ya ligiyi, kupitiriza zomwe idachita m’ndime yoyamba.

Timuyi idachapa Mafco ku Dwangwa komwe ndime yachiwiri ya ligiyi idakakhazikitsidwa. Bullets idapambana 1-0 ndipo pano yaonjezera mapointi kufika pa 35.bullets_celeb

Bullets ili ndi mapointi 7 pamwamba pa Azam Tigers, yomwe ili ndi mapointi 28. Koma Azam yamenya magemu ochuluka ndi imodzi kuyerekeza Bullets.

Azam idalepherana mphamvu ndi Kamuzu Barracks komanso Epac FC kuti ibwerere ku Blantyre ndi mapointi awiri kuchokera ku Lilongwe.

Mmodzi wa makochi a timu ya Bullets, Mabvuto Lungu, adati chomwe akufuna kuchita n’kuteteza mbiri yawo yosagonja.

Bullets sidagonjepo m’ndime yoyamba ya ligiyi.

“Matimu onse akonzekera zofuna kugonjetsa Bullets, ndipo akubwera mokonzeka kuti akwaniritse zomwe akufuna. Komabe tiyesetsa kuti mbiri yathu isasinthe,” adatero Lungu pouza Tamvani.

Mawa timuyi iswana ndi Red Lions pa Kamuzu Stadium. M’ndime yoyamba Bullets idalepherana mphamvu ndi timuyi 1-1 ku Zomba.

Timu yomwe Bullets imalimbirana nayo ufumu mumzinda wa Blantyre, ‘Mighty’ Be Forward Wanderers, yayamba moipa m’mdimeyi pamene idagonja ndi Civo United 1-0 pa Kamuzu Stadium sabata yatha.

Lero Wanderers, yomwe ili ndi mapointi 26, ndipo ili pa nambala 5, pam’ndandanda wa momwe matimu akuchitira m’ligiyi, ichapana ndi Kamuzu Barracks, yomwe ili ndi mapointi 23. Masewerowo ali pa Kamuzu Stadium.

Matimu ena amene ayamba molakwika ndi Dedza Young Soccer, yomwe idagonja ndi Red Lions. Mawa Young Soccer ndi Silver Strikers pa Silver Stadium.

Anyamata a ku Dedzawa ali panambala 11 ndi mapointi 15.

FISD Wizards nayo yayamba ndi kulira pamene idaswedwa ndi Civo 1-0 pa Kamuzu Stadium.  Lero FISD itengetsana ndi Moyale ku Mzuzu ndipo mawa ikutikitana ndi Mzuni FC pabwalo lomwelo.

FISD ili kunsonga kwa ligiyi ndi mapointi 9 okha. Mzuni ili panambala 15 ndi mapointi 11 pamene Moyale ili pa nambala 10 ndi mapointi 19. Mzuni ndi Moyale onse adaswedwa ndi Silver sabata yathayi.

Nayo Airborne Rangers idathotholedwa nthenga n’kugwa itatibulidwa ndi Blue Eagles 3-0. Lero Airborne ikulandira Epac ku Dwangwa pa Chitowe. Timuyi ili ndi mapointi 13 ndipo ili panambala 12, pamene Epac ili panambala 13 ndi mapointi 12.

Lero maso akhale pa Kamuzu Stadium ngati Bullets ipitirire kuchita bwino pamene ikuswana ndi mikango ya ku Zomba, Red Lions. 

Related Articles

Back to top button
Translate »