Chichewa

Bungwe lilangiza alimi kubzala mbewu zopirira

Listen to this article

 

Malingana ndi kabweredwe ka mvula ya masiku ano, akatswiri alimbikitsa kuti alimi asamangoganiza za mbewu zamakono koma mbewuzo zizikhala zopirira kuchilala zomwe akuti zili ngati inshuransi kwa mlimi.

Lanena izi ndi bungwe lolimbikitsa kutukula ulimi wa trigu ndi chimanga ku mmawa ndi kummwera kwa Afrika la International Maize and Heat Improvement Centre (CIMMYT) lomwe lakhazikitsa polojekiti ya zaka 4 yotukula mbewu zopirira kukagwa ng’amba.

Mkulu wa bungweli Dr Kennedy Lweya, adati mbewu zamakono zopirira ku ng’amba zili ndi ubwino waukulu kuposa mbewu zamakono chabe zomwe alimi ambiri amalima chifukwa ng’amba ikagwa zimaonongeka.

Mlimi kusamalira mmera m’munda wachimanga: N’kofunika kusankha mbewu yopirira kuchilala kuti zokolola zichuluke
Mlimi kusamalira mmera m’munda wachimanga: N’kofunika kusankha mbewu yopirira kuchilala kuti zokolola zichuluke

“Zokolola zimachuluka ndi 40 pa 100 iliyonse mlimi akabzala mbewu zamakono zopirira ng’amba. Mwachitsanzo, kubzala mbewu yamakono pamalo amodzi, mbewu yamakono yopirira ng’amba penapo, makololedwe ake safanana ngakhale zochitika paminda yonse zitafanana,” adatero Lweya.

Iye adati ng’amba ikagwa, mbewu zopirira ng’amba zimalimba mpaka kucha ngakhale kuti kucha kwake kumakhala kosafika momwe zingakhalire kutapanda kugwa ng’amba.

Iyi ndiyo akuitcha inshulansi kwa mlimi chifukwa zingavute maka amakhala ndi chiyembekezo chokolola kangachepe kusiyana ndi momwe zingakhalire mlimi atabzala mbewu yosapirira ng’amba.

“Chomwe tikutanthauza n’chakuti mlimi azibzala ndi chikhulupiriro chakuti pavute, pasavute adzakolola pantchito yomwe adagwira chifukwa polowetsa paliponse munthu umayembekezera zipatso.

“Nzowawa kuti munthu waononga ndalama, mphamvu ndi nthawi yako, pamapeto pake nkudzangopeza misinde yokhayokha popanda chimanga ngakhale chimodzi,” adatero Lweya.

Mkulu woyendetsa polojekitiyi, yomwe akuitcha Malawi Improved Seed Scaling Technologies (MISST), Willie Kalumula, adati mbewu zamakono zopilira ng’amba zilimo kale m’dziko muno ndipo cholinga cha polojekitiyi ndi kulimbikitsa alimi kubzala mbewuzi.

Iye adati cholinga china cha polojekitiyi n’kupititsa patsogolo kupekeza ndi kagwiritsidwe ntchito ka mbewuzi, zomwe zikufika kumene pamsika ndi kulimbikitsa njira zamakono za malimidwe.

“Kulima mbewu zimenezi kuli ndi ubwino waukulu kwambiri. Akatswiri adachita kafukufuku ndi kupeza kuti mvula ikagwa bwino, mbewu zopirira ng’amba zimachita bwino koposa ndipo ikapanda kugwa moyenera mlimi amakololabe ndithu,” adatero Kalumula.

Iye adati mbewuzi ndiye yankho lenileni lolimbana ndi njala komanso umphawi ndi kutukula miyoyo ya Amalawi, ntchito yomwe unduna wa zamalimidwe ukugwira.

Chaka chatha, mbewu zambiri zidafota osacha ng’amba itagwa mkatikati mwa mvula ndipo alimi ambiri ali pachiopsezo cha njala chaka chino, koma Kalumula adati alimiwa akadabzala mbewu zamakono zopirira ng’amba, vutoli silikadaoneka.

Iye adati pali mndandanda wa mbewuzi womwe watsimikizidwa kale ndipo alimi akhoza kuupeza pofunsa kubungweli kapena alangizi a zamalimidwe a m’dera lawo ndipo adzauzidwa komwe angazipeze. n

Related Articles

Back to top button