Chichewa

Bungwe lilimbikitsa ulimi wa akalulu

 

Akalulu ndi mtundu wa ziweto zing’onozing’ono zomwe alimi ambiri amanyalanyaza kuweta koma katswiri paulimi wa ziweto zosiyanasiyana, Sute Mwakasungula, wati ulimiwu ndi wopindulitsa.

Mwakasungula, yemwe ndi mkulu wa bungwe lomwe limagwira ntchito ndi alimi a ziweto aang’ono la Small Scale Livestock and Livelihoods Programme (SSLLP) akuti ulimi wa akalulu suboola m’thumba ndipo uli ndi ubwino wochuluka.

Muli chuma: Akalulu savuta kudyetsa
Muli chuma: Akalulu savuta kudyetsa

Kupatula kuchita ndiwo pakhomo, mkuluyu adati akalulu amabweretsa ndalama komanso mlimi amapindula ndi manyowa ochokera m’khola la akalulu ngakhale kuti iye amalowetsa ndalama zochepa.

“Choyamba, akalulu savuta kudyetsa chifukwa amadya zopezeka mosavuta.

Kusamala kwakenso, monga kumanga khola ngakhalenso kunyamula n’kosavuta chifukwa cha msinkhu wake,” adatero Mwakasungula.

Iye adati chisamaliro chakathithi ndiye chinsinsi cha phindu paulimi wa akalulu chifukwa kulephera kutero, akalulu amagwidwa matenda kapena kujiwa ndi zinyama zolusa.

“Khola la akalulu limafunika kukhala labwino. Akalulu amafuna chitetezo chachikulu kunyengo monga dzuwa, mvula ndi kuzizira.

“Amafunikanso chitetezo kunyama zolusa monga njoka, agalu, afisi ngakhalenso makoswe. Komanso safuna kusokonezedwa ndi phokoso,” adatero Mwakasungula.

Iye adati mbewu ya akalulu imapezeka mosavuta m’malo a zaulimi monga kusukulu ya ukachenjede ya Bunda, nthambi za boma zokhudzidwa ndi ulangizi wa zaulimi ngakhalenso alimi ena a akalulu.

Mwakasungula adati nkhani ina yaikulu pa ulimiwu yagona pa katetezedwe kumatenda, makamaka pokhala tcheru nthawi yosankha akalulu oweta.

“Nthawi zonse mlimi ayenera kuonetsetsa kuti akalulu sakuchucha m’mphuno, alibe zilonda m’makutu, kumapazi ndi malo obisika. Mwachidule, pogula akalulu oweta, gulani komwe muli nako chikhulupiriro kuti kulibe matenda,” adatero Mwakasungula.

Mkuluyu adati madzi ndi ofunika kwambiri pankhani yodyetsera akalulu mwakuti m’khola mumayenera kukhala madzi nthawi zonse chifukwa kalulu mmodzi ndi ana ake amamwa malita awiri patsiku.

Iye adaonjeza kuti pali zakudya zina zosayenera kudyetsa akalulu monga zakudya zomwe zaunga ndere, masamba a mbatatesi, masamba a mabilinganya ndi masamba a chinangwa.

Mwakasungula adati pofuna kusintha chakudya cha akalulu, pamafunika kusintha pang’onopang’ono osangoti kamodzin’kamodzi modzidzimutsa chifukwa kuteroko kumasokoneza m’mimba mwa akalulu ndipo akhoza kudwala n’kufa.

Related Articles

Back to top button