Chichewa

Bushiri adatidandaulira—HRCC

Listen to this article

Mkati mwa sabatayi mwachitika nkhani zikuluzikulu koma imodzi yomwe yamanga nthenje ndiyo ya banja la mneneri Shepherd ndi Mary Bushiri, atsogoleri a mpingo wa Enlightened Christian Gathering (ECG). Bushiri ndi mkazi wakeyo adamangidwa ku South Africa kumene amakhala ndipo atapatsidwa belo, Bushiri adathawa m’dzikolo Lachitatu sabata yatha kubwera kuno kumudzi. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Robert Mkwezalamba mmodzi mwa akuluakulu omwe alankhulapo ndipo ndi mkulu wa bungwe la Human Rights Consultative Committee (HRCC) komanso wapampando wa mgwirizano wa mabungwe amene mmbuyomu adadzudzula momwe milandu ya Bushiri idayendera ku South Africa. Adacheza motere:

Mkwezalamba: Tidapempha tikumane ndi a ku South Africa

Choyamba nkhaniyi ikukukhudzani bwanji?

Ife ngati mabungwe owona zaufulu wa anthu m’dziko muno takhala tikutsatira bwinobwino nkhani iyi ya banja la Bushiri yemwe tikudziwa kuti ndi wa bizinesi komanso mneneri yemwe adayambitsa mpingo wa ECG. Ife timamenyera ufulu wa anthu, utsogoleri otsatira malamulo komanso chilungamo ndipo mukaona nkhani ya banjali, ikukhudza zonsezi n’chifukwa chake ifeyo tachiona cha nzeru kulankhulapo.

Mukudziwapo chiyani za banja la Bushiri ndipo dandaulo lanu ndi lotani?

Choyamba, mneneriyu adatipeza ife amabungwe mu April 2018 ndi dandaulo loti amaopsezedwa kuti aphedwa ndi nzika zina ku South Africa komwe amakhala, adadandaula zambiri monga kuchitiridwa nkhanza zosiyanasiyana, kunyogodoledwa komanso kukakamizidwa kuchita zinthu makamaka ndi nthambi zachitetezo kumeneko. Tidatuma nthumwi ku South Africa mu June 2018 kukafufuza ndipo tidapeza kuti Bushiri amanena zoona. Tidayesa njira zosiyanasiyana kukambirana ndi boma la South Africa mpaka tidawapatsa maina a anthu omwe amakhudzidwa koma sizimayenda. Lina mwa pempho lathu kudziko la South Africa lidali loti atitsimikizire kuti Bushiri azipatsidwa mwayi onse omwe munthu aliyense amayenera akafunika kuyankha mlandu uliwonse komanso kuti anthu omwe amakhudzidwa ndi kumuopsezawo asamatenge nawo gawo pankhani zake zonse. Mwezi wa October 2020 tidapempha kuti tikumane ndi nthambi ya zakafukufuku ku South Africa ndipo adatiuza kuti atipatsa tsiku koma yankho lisadabwere tidangomva kuti Bushiri ndi banja lake awamanga ndipo anthu omwe aja akukhudzidwa n’kumuopseza aja adali m’gulu lomumangalo.

Mwaphunzirapo chiyani pa zomwe akudutsamo Bushiri ndi banja lake?

Kuchoka kumangidwa kwa banja la Bushiri koyamba mu 2019, taonapo zinthu zingapo. Choyamba, banjalo likuweruzidwa ndi ofalitsa nkhani, akuluakulu ambiri a boma la South Africa adaonetsa poyera kunyansidwa kwawo ndi banjalo kufikira pomapempha kuti Bushiri ndi banja lake abwerere ku Malawi, mipingo yambiri ndi abusa ake komanso nthambi zambiri kumeneko zakhala zikumema anthu kuti aukire Bushiri ndi mpingo wake, nthambi za boma kumeneko zakhala zikupeleka mpata kwa osagwirizana ndi Bushiri kuti azipelekera zida zokhomelera banjali mwachitsanzo mbusa wina kumeneko otchedwa Mboro adanena poyera kuti samafuna kuti banja la Bushiri lituluke pa belo koma chifukwa adapemphedwa ndi a kubanja la Bushiri adavomera kuti akhoza kutuluka ndipo tsiku lomwelo pa 4 November 2020 banjali lidatuluka pa belo. Kuwonjezera apo, akuluakulu a m’boma la South Africa kuphatikizapo nduna zaboma akhala akuthilirapo ndemanga pa nkhani zoti zili m’khoti kuphatikizapo kulankhula poyera kuti Bushiri ndi kapsala oyenera kulangidwa, kutseka mabuku ake a kubanki kwa chaka chatunthu pa nkhani yoti amangoti akufufuza. Zimenezi zikuonetsa kuti pali kampeni komwe akumusungira Bushiri kwawoko makamaka mukamamva zomwe akunena kuti “Bushiri abwere adzazione kuno.”

Mukuona ngati Bushiri adathawiranji ku South africa n’kubwerera kuno?

Kwaife titakhala pansi n’kuunguza mofatsa tapeza kuti ganizo la Bushiri longobwerera kumudzi lidafika kaamba ka nkhanza ndi kuopsezedwa komwe amalandira m’dziko la South Africa. Iye amafuna kuteteza moyo wake ngati momwe akunenera mwini wake. Nkhawa ndi chiopsezo chomwe Bushiri akudandaula zisatengedwe mwa masanje makamaka potengera kuti tikukamba za dziko lomwe lili ndi mbiri ya kuphana mwachisawawa. Ife ngati omenyera ufulu tikufuna Bushiri akhale moyo kuti adzayankhe milandu yomwe akunenayo yekha ndipo chilungamo chidzaonekere poyera. Koma panopa tikupempha dziko la South Africa kuti lisatembenuze milandu ya Bushiri poyikankhira koti wathawa ayi koma kuti apitirize ndi milandu yomwe akumuzenga kale komanso akuonetsetsa kuti chitetezo chake n’chokhwima. Boma la South Africa limve nkhawa za Bushiri ndi za mabungwe omenyera ufulu a ku Malawi kuno.

Tsono mwati dziko la Malawi likugona pankhaniyi, mukutanthauzanji?

Ngakhale tikumvetsetsa kuti dziko la Malawi lasankha kusalowerera pankhani yokhudza malamulo, n’zokhumudwitsa kuti onse boma la Democratic Progressive Party (DPP) komanso boma lomwe lilipoli adasankha kukhala mbali yongoonerera kuti zitha bwanji. N’zosamveka kuti nzika ya dziko payokha ingalimbane ndi dziko lalikulu ngati South Africa yokha popanda dziko lake kuthandizapo munjira iliyonse. Ngati dziko la Malawi silingalowerere pa nkhani ya munthu ngati Bushiri ndiye kuti Amalawi ambiri omwe akukhala m’maiko ena angokhalira chisomo cha Mulungu.

Pomaliza mawu anu ndi wotani?

Ndimalize ndi pempho loti kuti nkhaniyi iyende bwino, dziko la Malawi lionetsetse kuti banja la Bushiri latsimikiziridwa mokwanira zachitetezo chawo komanso kuti mlandu wawo udzayenda mwachilungamo ndipo izi n’zoyenera kusayinirana, dziko la South Africa lichotse anthu onse omwe akukhudzidwa ndi kuopseza Bushiri ndipo ozenga mlanduwo akhale anthu okhulupilika, dziko la Malawi lisapupulume kutumiza Bushiri ku South Africa pokhapokha zonse zili mmwambazi zitatsimikizika, zonsezi zikatheka dziko la Malawi litumize nthumwi zake zomwe zikaime limodzi ndi Bushiri kuti mlandu wake ukayendedi mwachilungamo komanso tipemphe dziko la South Africa kuti anthu ake asazunze Amalawi chifukwa chotsatira kapena kupemphera mpingo wa Bushiri.

Related Articles

Back to top button
Translate »