Chichewa

Bwalo lilanga mphunzitsi wochimwitsa mwana

 

Bwalo la milandu la majisitireti la Mzuzu lapeza mphunzitsi wina wolakwa pamlandu wochimwitsa mtsikana wosakwana zaka 16, komanso kupereka mankhwala ochotsera pathupi pomwe adampatsa. Bwaloli likuyembekezeka kupereka chilango chake mawa pa 22 February.

Lachinayi sabata yatha bwaloli lidamva kuti Mtendere Phiri, wa zaka 31, yemwe kwawo ndi ku Bembeke, T/A Kachindamoto, m’boma la Dedza, adayamba kugonana ndi mwanayu mwezi wa April chaka chatha.

ARREST

Bwaloli lidamva kuti Phiri, yemwe amaphunzitsa pasukulu ina yapulaimare ku Ekwendeni m’boma la Mzimba, adanyengerera mtsikanayu kuti akakana chibwenzi, asiya kuphunzitsa pasukulupo ndipo apita kwina.

“Izi zidamukhudza mtsikanayu ndipo posafuna kuti mphunzitsiyo achoke, adamulola ndipo ankapita kunyumba kwake mkazi wake akapita ku Mzuzu kwa mayi ake,” adawerenga majisitireti Agness Gondwe.

Apatu nkuti Phiri yemwe adavala malaya ofiira, ali wera m’chitokosi cha bwalo la milandu, naye mkazi wake ali poteropo kumvetsera majisitiretiyu.

Ndipo iye adapitiriza kuti malinga ndi umboni womwe udaperekedwa m’bwalolo masiku apitawo, awiriwa ankachita zadamazi kuchipinda kwa mphunzitsiyu.

Gondwe adati mtsikanayu adauzanso bwalolo poperekera umboni wake kuti zadamazi zidachitika kosawerengeka ndipo Phiri adamuuza kuti akadzadutsitsa mwezi osasamba adzamudziwitse msanga.

Iye adati mwezi wa July msikanayu adaima ndipo atamudziwitsa mphunzitsiyu, sadachedwe koma kumupatsa mapilitsi awiri a Brufen komanso a Bactrim zomwe sizidaphule kanthu chifukwa pathupipo sipadachoke.

Majisitiretiyu adati apa mtsikanayu adapita kutchuthi mumzinda wa Mzuzu komwe pobwerera m’mwezi wa September mayi ake

adamuzindikira kuti adali ndi pathupi.

Iye adati mayi a mtsikanayu adamuuzitsa kuti asachotse mimbayo, koma izi sizidathandize chifukwa atakumananso ndi mphunzitsiyo adamuuza kuti ngati atasunge pathupipo zake zida.

“Malinga ndi umboni womwe udaperekedwa m’bwalo lino, Phiri adamuuza mtsikanayo kuti apite naye kuchipatala cha Banja La Mtsogolo (BLM) akamuchotse, koma atakana adakagula mankhwala asanu ndi anayi kuchipatalachi,” adatero Gondwe.

Mtsikanayu atamwa, pathupipo padachokadi pakati pa usiku ndipo adakataya zomwe zidatulukazo m’chimbudzi.

Koma madzi adachita katondo pomwe mtsikanayu adayamba kugudubuzika ndi ululu wa m’mimba ndipo adaulula kwa mayi ake kuti mphunzitsiyo ndiye adali mwini nkhaniyi.

Apa adathamangira naye pachipatala chachin’gono cha m’derali komwe adamutumiza kuchipatala chachikulu cha Mzuzu Central komwe adamuchotsa zotsalira.

Ndipo mayi a mwanayu molimbikitsidwa ndi a mabungwe adakaman’gala kupolisi komwe adamutsekera Phiri pa September 23 chaka chatha.

Christon Ghambi, yemwe akuimira mphunzitsiyu, adaseketsa bwaloli pomwe adalipempha kuti limuganizire phiri posampatsa chilango chokhwima poti adapereka mankhwala ochotsera pathupiwo kuti tsogolo la mwanayu lisaonongeke.

Phiri adziwa chilango chake mawa pomwe bwaloli likuyembekezeka kupereka chilango choyenera kwa mphunzitsiyu. n

Related Articles

Back to top button