Nkhani

CHAKA CHA 2014 CHALIZA AMALAWI

Listen to this article
Chifukwa cha umphawi ambiri akulephera kugula ngakhale patapata
Chifukwa cha umphawi ambiri akulephera kugula ngakhale patapata

Sizidayende kumbali ya chuma—Kaluwa

Palibe chikuchitika! Uku ndiko kuwunguza kwa akadaulo pandale komanso pa zachuma pa momwe chaka cha 2014, chomwe chikutha Lachinayi likudzali, chidayendera.
Akatswiriwa, amene ndi Prof. Ben Kaluwa ndi Joseph Chunga a ku Chancellor College (Chanco), ati boma silikuchita mokwanira kuti libwezeretse zinthu zomwe zidasokonekera ndipo mmalo mwake Malawi wayambanso kubwerera mmbuyo.
Ndemangazi zikudza pamene chaka cha 2014 chidakumana ndi mavuto osasimbika amene adakhodzokera chifukwa cha ganizo la abwenzi a dziko lino loleka kutithandiza.
Dziko la Malawi lakhala likulandira K4 pa K10 iliyonse ya ndondomeko ya zachuma kuchokera kwa abwenzi ake, koma lero ndi mbiri chabe chifukwa abwenziwa adafungata thandizo lawo kaamba ka kubedwa kwa ndalama m’boma.
Mu September 2013, aliyense adadzidzimuka kumva kuti yemwe adali pa mphika wa ndondomeko ya zachuma m’dziko muno, Paul Mphwiyo, amuthira machaka.
Kuomberedwa kwa Mphwiyo kudavumbulutsa zambiri pamene chuma cha boma chidayamba kusololedwa. Kusololedwaku kudakhodzokera mu January 2014 zomwe zidachititsa abwenziwa kuti aimike manja n’kusiya zothandiza dziko la Malawi.
Monga akunenera Kaluwa, kubedwa kwa ndalamaku ndiko kwakolezera moto kuti Amalawi akhale pampanipani.
“Mwaona momwe Amalawi avutikira, zinthu zikungokwera chifukwa ndalama yomwe timagulira katundu wokwanira pabanja pathu kwa mwenzi wonse, lero ikugula katundu wochepa,” adatero Kaluwa.
Mu August, bungwe lomwe limaona momwe moyo ukuyendera la Centre for Social Concern (CfSC) lidatulutsa mndandanda wa momwe zinthu zakwerera zomwe zimachititsa kuti ndalama yogwiritsira ntchito pamwezi ikhale yokwera.
Bungweli lidati anthu awonjezera ndalama yomwe amagwiritsira pamwezi ndi K2.7 pa K100 iliyonse yomwe amagwiritsira ntchito.
Izi zimatanthauza kuti munthu wokhala m’mizinda ya Zomba, Blantyre, Mzuzu ndi Lilongwe amayenera ayambe kugwiritsa ntchito K120 000 pamwezi kuchoka pa K117 000.
Kutsatira izi, mu September chimanga chidakwera ndi K2 pa K10 iliyonse. Mu November shuga adakwera ndi K8 pa K100 iliyonse komanso zakumwa zidakwera kutsatirana ndi kukwera kwa mayunitsi a TNM ndi Airtel.
Koma Kaluwa akuti ndi zotheka kuti dziko lino libwerere m’chimake ngati litakonza zosokonekera.
“Taonani momwe nkhani zophana zikuchitikira? Anthu amene angabweretse bizinesi m’dziko muno sangakhale chifukwa cha nkhani zachitetezo zomwe zasokonekera,” adatero Kaluwa.
Naye Chunga adati kupatula zisankho zomwe zaonetsa kuti Amalawi akhwima pandale, dziko lino likubwerera mmbuyo.
“Posakhalitsapa timamva za kusokonekera kwa boma lapita lija ndiye sungayembekezere kuti tiyambenso kuziona zomwe zija,” adatero Chunga. “Izi zikungosonyeza kuti tikubwerera mmbuyo.”
Amalawi akhala akudzudzula mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika kuti wayamba tsankho posankha nduna zambiri za chigawo chammwera zomwenso zakhala zikuchitika mmbuyomu.
M’chakachi, nkhani yomwenso idazunguza Amalawi ndi mavuto amadzi amene adachititsa anthu kufuna kuchita zionetsero zokwiya ndi mabungwe amene amayendetsa za madzi.
Ngakhale madzi lidali vuto, komabe bungwe loyowona za madzi la Water Board lidakweza mtengo wa madzi ndi K5 pa K10 iliyonse.
Nalo bungwe loyendetsa zamagetsi la Escom lidakweza magetsi ndi K3.7 pa K10 iliyonse. Nawonso mafuta agalimoto ndi palafini adakwera mtengo.
Izi zachititsa kuti anthu amve kuwawa mu 2014. Ngakhale ino ndi nthawi yachisangalalo, anthuwa akuti palibe chosangalalira.
Lackson Nkhoma wa m’mudzi mwa Dzinjiriza kwa T/A Mpando m’boma la Ntcheu akuti walira mokweza chaka chino.
“Ndimagulitsa zakumwa, adatikwezera msonkho wa pachaka kuchoka pa K4 500 kufika pa K7 500. Phindu palibe, ndasowa ndi ndalama yoti ndisangalale ndi ana nthawi yachisangalaloli,” adatero Nkhoma.
Basitiyana Chizinga wa m’boma la Mulanje koma akukhala mumzinda wa Blantyre, akuti mavuto ndiwosakamba.
“Ndimagulitsa mayunitsi, nafenso tidakwezeredwa msonkho wogulitsira mayunitsi pachaka kuchoka pa K4 000 kufika pa K7 000. Eeh! chaka chinochi, ayi ndalira. Bolaninso 2013 yomwe ija,” adadandaula Chizinga.
Nyakwawa Kuziona ya m’boma la Neno ikuti anthu ake avutika kaamba ka kusowa kwa madzi komanso kusowa chipatala.
“Tidayembekeza kuti ndi kusintha kwa boma anthu anga apumulako kumavuto amene timawaona monga kusowa kwa madzi, sukulu ndi chipatala zili kutali. Koma awo adali maloto chabe,” adatero Kuziona. 

Related Articles

Back to top button