Nkhani

Chaka cha anamwino ku Salima lero

Listen to this article

Kuli chaka lero ku Salima pamene anamwino m’dziko lino akukondwerera tsiku lokumbukira ntchito yawo pa dziko lapansi.

Anamwino padziko lonse amapatula tsiku la 12 May chaka chili chonse ati popereka ulemu kwa katswiri wina wakale yemwe anayambitsa unamwino wa makono, Florence Nightingale yemwe anamwalira m’chaka cha 1910 ali ndi zaka 90.

Mkulu wa bungwe la anamwinowa la National Organisation of Nurses and Midwives of Malawi (NONM), Dorothy Ngoma, anauza atolankhani kuti chikondwerero cha chaka chinochi chilunjika pa mutu womwe ukulimbikitsa zotengapo mbali polimbana ndi matenda ndi imfa.

Ngoma anatambasula kuti ngakhale dziko lino limadziwa zofooka zambiri pantchito za umoyo, magawo ochepa okha a anthu ndi amene amayesa kuchitapo kanthu.

Iye anati izi zikukweza chiwerengero cha odwala komanso omwalira kaamba ka matenda m’dziko muno.

“Mwachitsanzo, bungwe loona za umoyo pa dziko lonse la World Health Organization limalimbikitsa kuti namwino aliyense adziyang’anira odwala osapyolera zana limodzi koma kuno kwathu namwino akumasamalira odwala oposa 3800 kaamba kuchepa kwa anamwinowa.” Anatero Ngoma.

Pa mwambo wa ku Salimawu, anamwino onse akuyembekezeka kukagawana ntchito zosamalira odwala pa chipatala cha m’bomalo komanso kusamalira mabwalo a sukulu ya sekondale ya Salima, ati pochitira umboni kuti ntchito za umoyo zingathe kupita patsogolo ngati manja angachuluke.

Kukakhalanso kupereka mphoto kwa ogwira ntchito za umoyo omwe achita bwino m’chakachi n’cholinga chowalimbikitsa komanso kukuza chidwi mwa anzawo.

Related Articles

Back to top button