Chichewa

Chaka chomwe zogwiririra Ana ndi amayi zanyanya

Listen to this article

November 21 2020. Kulira kwa khanda la miyezi 5 kudamveka m’boma la Zomba. Khandali silimalira chifukwa cha njala kapena kuti ladzionongera ayi. Koma lidagwiririridwa ndi bambo wina wa zaka 31.

Bamboyu Muderanji Kanjira akuganiziridwa kuti adagwiririra khandali atakalitenga kuchoka kwa makolo ake kuti acheze nalo. Kanjira amakhala nyumba zoyandikana ndi makolo a khandalo.

Ngati pali nkhani imene yayala nthenje m’chakachi ndiye ndi yogwiririra makanda, ana, atsikana, amayi ndi ziweto.

Kaliya: N’zodandaulitsa

Chiwerengero chikuonetsa kuti kuchoka mwezi wa January kufika October, ana oposa 1 738 agwiriridwa m’dziko muno poyerekeza ndi 1 440 omwe adagwiririridwa chaka chatha.

M’chiwerengerochi muli mwana wa zaka 10 yemwe moyo wake wasokonekera kaamba kogwiriridwa  mzinda wa Lilongwe.

Polankhula ndi Msangulutso, mayi a mwanayu adati ngakhale padutsa mwezi, mwanayu sakumasukanso posewera ndi amnzake.

“Nthawi zambiri akumangokhala ndwii! Malo ake obisika akumatupa akamathamangitsana ndi anzake,” adatero mayiyu.

Kuphatikiza apo, iye akudandaula kuti mwana wake akusalidwa ndi anzake omwe adamva za nkhaniyi.

“Ndingofuna mwana wanga atachoke m’dera lino n’kupita kutali kuti akayambenso moyo wina watsopano,” adatero mayiyo.

 Nawo mafumu akudabwa ndi kukula kwa mchitidwe wogwiririra m’madera awo.

Mfumu Chikumbu ya m’boma la Mulanje idati zikuchitikazi sizidachitikenso mbiri ya dera lake.

“Taganizani, kuchoka sabata yatha kudzafika ino ana awiri agwiririridwa m’dera mwanga. Wina wa zaka 10 wagwiririridwa ndi bambo wa zaka 35 pamene wa zaka 5, wagwiririridwa ndi wa zaka 21,” adatero Chikumbu.

Iye adati vuto lalikulu sizizimba, koma mankhwala wozunguza bongo omwe abambo ena akugwiritsa ntchito.

“Kale kudalibe zimenezi, koma panopa zawonjeza. Pakadali pano m’sitolo zina makamaka za anzathu ochokera ku China akugulitsa mankhwala wopereka chilakolako pogonana zomwe abambo ena akumamwa ndipo mphamvu ya mankhwalawo ikumathera pa ana,” adatero Chikumbu.

Chikumbu adapempha boma kuti likhazikitse mabwalo oti azizenga milandu m’mudzi ndi cholinga choti azipereka phunziro kwa anthu kudzera m’zilango zokhwama zomwe azipereka.

Mfumu Kachindamoto ya ku Dedza idati idamema anthu ake ndi cholinga chofuna kuthana ndi vutoli.

“Ndidapita ndekha kukagwira abambo ena omwe adagwiririra ana anayi n’kukawasiya ku polisi,” adafotokoza choncho Kachindamoto.

Wachiwiri kwa mneneri wa polisi Peter Kalaya adati ambiri mwa ogwiririra amati apalamula mlanduwo kaamba ka zizimba zomwe asing’anga amawapatsidwa kuti alemere kapena achire ku matenda.

“Pamene ena amapalamula mlanduwu akagwiritsa ntchito mankhwala ozunguza ubongo, komanso akamwa mowa mwauchidakwa,” iye adatero.

Malinga ndi Kalaya, ena amangoti Satana ndiye adawanyenga, kutanthauza kuti amalingalira ndi kukonzekera asadachite izi.

Kafukufuku wa Msangulutso m’chakachi waonetsa kuti kugwiririra sikudasiye mbali.

Pamene ana ena akugwiriridwa ndi aphunzitsi awo, ena akugwiriridwa ndi abusa awo.

Ana ena akugwiriridwa ndi apolisi omwe amawadalira kuti awateteza.

Koma chomvetsa chisoni kwambirinso n’choti ena mwa anawa adagwiriridwa ndi bambo awo owabereka, komanso owapeza ngakhalenso achibale.

Poona kuti vutoli lanyanya, boma lati likonzanso malamulo kuti opezeka olakwa pa mlandu wogwiririra azilandira zilango zokhwima komanso milandu yawo iziyenda msanga.

Nduna ya za chilungamo Titus Mvalo ndiyo idanena izi masiku apitawo m’boma la Rumphi patsiku lokumbukira ufulu wachibadwidwe wa anthu.

Womenyera ufulu wa anthu m’dziko muno Emma Kaliya, adati chakachi chidali chodandaulitsa ku nkhani zogwiririra.

Iye adati chachiwiri Amalawi akuyenera kuunikira bwino zomwe zikukulitsa mchitidwewu.

“Nthawi zina tikumva kuti ndi zizimba zomwe asing’anga akupereka kwa anthu kuti alemere.

Pothirirapo ndemanga pa zifukwa zomwe ambiri amagwiririra ana, katswiri pa nkhani za kaganizidwe pa sukulu ya ukachenjede ya College of Medicine, Chiwoza Bandawe, adati anthu ena amakhala  wosokonekera m’chikhalidwe zomwe  zimawachititsa kuona dzikoli mwachilendo, komanso osafuna kucheza ndi kuyanjana ndi anzawo.

Iye adati izi ndi zimene zimawachititsa kugwiririra ana.

Related Articles

Back to top button