Chichewa

Chaka ndi miyezi inayi ali m’chipatala osaimirira

Listen to this article

 

Maloto a Alineti Molosi wa zaka 15 odzakhala namwino akhoza kufera m’mazira ngati madotolo sakwanitsa kumuchiza nthenda yozizira miyendo yomwe idayamba msuweni wake atamubaya ndi mpeni.

Alineti akuti ululu omwe akusauka nawo panowu gwelo lake ndi chipatso cha ndimu chomwe amafuna kuthyolera mwana wa azakhali ake mumtengo omwe uli pakhomo pomwe msuweni wakeyo amakhala.

Iye adati ili lidali khumbo chabe chifukwa sadathyole chipatsocho ataona kuti pakhomopo padalibe munthu aliyense ndipo adabwerera kuti eni khomo akafika apite kukapempha koma mwatsoka msuweni wakeyo adamuona ndipo adamutsatira.

Alineti (wagona) pakama kuchipatala ndi mayi ake
Alineti (wagona) pakama kuchipatala ndi mayi ake

“Adafikira kundinena kuti ndaba mandimu ndipo ine ndikukana adatenga mpeni nkundibaya pakhosi kumbuyo ndipo kuchoka apo ndidadzazindikira ndili m’chipatala koma sindikumbuka momwe ndidabwerera,” adatero Alineti.

Padakalipano, msungwanayu watha chaka ndi miyezi 4 osayima kapena kukhala tsonga m’chipatala cha Kamuzu Central kaamba kakuti thupi lake lidazizira kuchokera mchiuno mpaka kumapazi.

Mai ake a Alineti, Leniya Molosi adati izi zidachitika mwezi wa August, 2014 m’mudzi mwa Nthanje T/A Malengachanzi ku Nkhotakota pomwe mwana wakeyo adakachita tchuthi kwa azakhali akewo.

Iwo adati msungwanayu adali mu sitandade 7 ndipo amachita bwino m’kalasi moti samakayikira kuti akadakwanitsa maloto odzakhala namwino.

“Ntchito ya unamwino amayifunadi chifukwa kuyambira kale ukamufunsa chomwe akufuna kudzakhala mtsogolo amanena za unamwino moti apa chisoni chikundipweteka kwambiri chifukwa m’chipatalamu akumaona anamwino tsiku ndi tsiku,” adatero Leniya.

Chomvetsa chisoni kwambiri nchakuti makolo ake a msungwanayu ali pa vuto la zachuma moti pocheza ndi Msangulutso sadabise kuti chilowereni m’chipatalamo, palibe m’bale yemwe adabwerako kudzawazonda kaamba kosowa mayendedwe.

Maiyu adandandaula kuti kuti kwa chaka ndi miyezi 4 tsopano sadaone amuna ake ndi ana ake ena 6 omwe adawasiya ku Nkhotakota ndipo sakudziwa kuti adzawonana nawo liti.

Msangulutso adalephera kulankhula ndi dotolo yemwe akuthandiza msungwanayu koma mayi akewo adati vuto lomwe dotoloyo adapeza ndi lakuti mpeniwo udakalasa mtsempha waukulu zomwe zidapangitsa kuti ziwalo zina zizizire.

“Tikungokhala muno sitikudziwa kuti tidzatuluka liti poti vuto lake likuoneka kuti ndi lalikulu. Nkhawa ina ndi ana anga omwe ali kunyumba ndi kumunda chifukwa ndimo timapezera chakudya ndi ndalama,” adatero Leniya.

Mneneri wa polisi m’boma la Nkhotakota Williams Kaponda adati ayambe kaye wafufuza m’mabukhu a kupolisi momwe nkhaniyi ikuyendera. n

Related Articles

Back to top button
Translate »