Nkhani

Chakwera akumbukira masiku 100 a Tonse

Listen to this article

Lolemba, mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera adali ndi mwambo wokumbukira kuti watha masiku 100 akulamula dziko lino. Pamwambo umene udachitika ku nyumba ya boma ya Kamuzu Palace ku Lilongwe, Chakwera adafotokoza zinthu 35 zimene wakwanitsa kuchita ndipo atolankhani komanso Amalawi adali kufunsa mtsogoleri wa dziko linoyu zina ndi zina. STEVEN PEMBAMOYO akusungunula mafunso ndi mayankho motere:

Chakwera: Tapanga zambiri

Tatiuzani kuti kodi masiku 100 oyambirira muulamuliro wanu mwaziona bwanji?

Amati fumbi ndiwe mwini koma pano tinena zenizeni momwe zilili. Ndikudziwa kuti Mmalawi aliyense payekhapayekha akutsatira momwe zinthu zikuyendera ndipo potengera momwe tayambira, n’zosabisa kuti tsogolo likuoneka. Mwina ndiyambe ndikunena kuti wina aliyense payekhapayekha abwerere mmbuyo pang’ono n’kuona kuti tidali pati nanga tsopano tili pati, tikatero tiona kuti dziko lathu likutsitsimuka ku mavuto omwe lidalimo. Kuyankha kwake mwachidule ndinene kuti masiku amenewa 100 oyambirira apereka chithunzithunzi cha Malawi watsopano owala.

Mwati tiunike mmbuyo, tangotipatsani chithunzithunzi kuti mmbuyomo mudali bwanji?

M’miyezi yapitayo boma lisadasinthe, dziko lino lidali ngati ngalawa yomwe imalowera kokamira ndipo idatsala pang’ono kumirako. Dzikoli lidafika pangati ngalawa yomwe amalinyero ndi anthu ena mmenemo adasiya kulabadira za anthu koma kufuna kudzilemeretsa okha, omwe amatsogolera adatayilira moti zimakhala ngati anthu omwe ali m’ngalawa n’kumatunga madzi kumathira m’ngalawa yomweyo kuti imire ndithu basi. Mukulandira malipoti a momwe anthu amabera m’boma lapitalo inu ndipo mukudziwa zomwe ndikutanthauza.

Mwachidule boma lanu lapanga chiyani m’masiku 100 ake oyambilira?

Tapanga maziko abwino okwaniritsira malonjezo athu a pakampeni. Aliyense akuona momwe anthu akutsatira malamulo, mwaona momwe tidaonjezerera ndalama ku bungwe lolimbana ndi ziphuphu (ACB) kusonyeza kuti taika mtima pankhani yolimbana ndi katangale, tidasankha nduna 31 motengera ndi kuthekera kwawo komanso mwaona posachedwa mabodi a makampani a boma omwe tasankha. Kumbali yotukula amayi ndi achinyamata mwaona tasitha dzina la nthambi yopereka ngongole ya Medf kukhala National Economic Empowerment Fund (Neef) kuti ipereke chithunzi chenicheni cha cholinga chake chifukwa mmbuyo muja anthu amangochitenga ngati kongotapa ndalama n’chifukwa chake mpaka pano ndalama zina sizidabwezedwe ndipo n’zovuta kulondoloza chifukwa amangopatsana ngongole popanda mutu weniweni. Tikanena za feteleza wotsika mtengo pulogalamu yake ndi iyi mwayiona kale m’bajeti ya 2020 mpaka 2021, tikupanga zinthu mwadongosolo kuti zikakhazikika kutsogoloko ena asadzayambirenso pansi koma adzangopitiriza chitukuko. Padakalipano tili mkati mosintha kagwiridwe ka ntchito m’boma kuphatikizapo kuchita chipikisheni cha anthu omwe adalowa ntchito mwachinyengo, tikukumana ndi mabungwe komanso anthu osiyanasiyana kumva maganizo awo pa zinthu zina ndi zina, sabata iliyonse mukukhala ndi mpata womva momwe zinthu zikuyendera kutanthauza kuti boma lathu ndi boma lochita zinthu pambalambanda. Tiyeni tiyendere limodzi ndipo tipatira limodzi zabwino.

Mwanena za mabodi a makampani aboma ndipo pali kulira kwakukulu akuti amayi mwawataya, pamenepo bwa?

Kuyankha kwake ndinene motere kuti posankha mabodi amakampani aboma timayendera mndandanda omwe tili nawo n’kumaona kuti kodi pamenepa omwe angayendetse kampani iyi bwino ndi anthu ati. Ndiye anthu asadaloze zala nkhani ya amayi tikuyenera kukambirana kuti kodi tidali ndi mndandanda wotani wa amayi. Monga ndidanena kale poyambirira penipeni, ine ndi anzanga kuutsogoleri kuno timafuna anthu muzithandizira tikamapanga zinthu, mwachitsanzo amene akudziwa za amayi oti akhoza kuyendetsa zinthu zina atipeze ndi maina amenewo kuti ifenso posankha maudindo ena ndi ena tizikhala ndi chitsime chakuya chosankhamo amayi oti akagwire ntchito zikuluzikulu zaboma.

Achinyamata maso ali pantchito 1 miliyoni zomwe mudalonjeza zija, muwauzanji lero?

Tikamati ntchito 1 miliyoni anthu azimvetsetsa kuti si nkhani ya lero ndi lero ayi. Si kuti polonjeza ntchitozo ndiye kuti zidali zilipo kale ayi koma tikupanga ndondomeko zoti ntchitozo zipezeke ndipo iyi si nkhani ya boma lokha ayi koma munthu aliyense. Mu Malawi muno, boma ndilo limalemba anthu ambiri ntchito pomwe sizimayenera kukhala choncho, makampani ndi mabizinesi amayenera kuti akhale pachinyezi choti ziziyenda kuti azilemba anthu ambiri ntchito. Izi ndi zina mwa zomwe tikupanga kuti makampani ndi mabizinesi akhale ndi kuthekera kotero. Ndikhoza kukutsim-ikizirani kuti anthu onse ogwira ntchito m’boma sapitirira 200 000 ayi. Izi zikutanthauza kuti ngakhale titachotsa onse lero, sikuti m’bomamo mupezeka ntchito 1 miliyoni ayi, apezekapobe achinyamata ambiri omwe sapeza nawo mwayi ndiye nkhani yagona podekha kuti zinthu zitiyendere bwino.

Tipite kumaphunziro, ophunzira ambiri a sukulu zaukachenjede akuthamangitsidwa chifukwa chosowa fizi. Kodi boma lanu liwathandiza motani ophunzira oterowo?

Ndafunsidwako mafunso ambiri pankhani imeneyo ndipo ndi nkhani yoona koma monga ndakhala ndikunena, pali zinthu zina sumangopanga pompopompo zimafunika pulani yabwino. Koma kunena zoona nkhani ya maphunziro si nkhani yosereula chifukwa chilichonse chimafuna maphunziro kuti chiyende ndipo ngati tilidi dziko lofuna kutukuka, tikuyenera kutukula maphunziro. Ngati boma tiyesetsa kupanga zoti sukulu zizikhala ndi zoyenereza zonse kuti mavuto ngati amenewo asamachuluke koma tifunabe nthawi kuti zotere zifike pokhazikika n’kumaoneka ndi maso. Komanso anthu ndi makampani akuyenera kugwirana manja ndi boma potukula zinthu ngati maphunziro osangolisiyira lokha boma ayi.

Pomaliza, anthu amadabwa chomwe mafumu amapitira kumsonkhano waukulu wa maiko (Unga), m’boma lanu ayembekezerenji Amalawi?

Cholinga cha misonkhano imene ija ndi kukambirana zokhudza zitukuko m’maiko ndiye kumakhala nkhani zambiri kumene kuja zofunikanso anthu osiyanasyana ozitsata bwino. Mumadziwa inu kuti m’dziko muno muli mafumu ophunzira bwino ndipo otsata zinthu kwambiri? Kuyambira lero mukawona mafumu muzidziwa kuti ena mwa iwo adachita kusiya ntchito zapamwamba kukatumikira anthu awo kwawoko ndiye akamapita kumisonkhano yakunjayo amakhala kuti pali gawo lomwe asankhidwira kuti akatiimire kunjako.

Related Articles

Back to top button