Nkhani

Chakwera, Nankhumwa akhambitsana

Chilinganizo chomwe chidaikidwa pofuna kuti mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera akayankhe mafunso m’Nyumba ya Malamulo chidasanduka mtsutso pakati pa iye ndi mtsogoleri wa mbali yotsutsa boma m’Nyumbayo Kondwani Nankhumwa.

Mtsogoleri wa dziko linoyu adayembekezeka kuti akayankhe mafunso omwe aphungu adali nawo pa zomwe adalankhula Lachisanu sabata latha pa za pamene dziko lino likuyendera.

Chakwera: Adziwa liti?

Koma atayamba kulankhula m’nyumbayo, Chakwera adaoneka kuti akutsamira kwambiri pa zomwe adalankhula Nankhumwa poyankhapo pa uthengawo.

Mwa zina zomwe adakhudzapo mu uthenga wake m’Nyumbayo, Nankhumwa adafunsa boma kuti lipereke ndalama zapadera kwa aphunzitsi pamene sukulu zatsegulidwansomu ati ponena kuti iwo akuika miyoyo yawo pa chiswe ku nthenda ya Coronavirus (Covid-19) yomwe yavutitsa pa dziko lonse lapansi.

Koma Chakwera adati pa anthu onse, a Nankhumwa sadali woyenera kuti apereke uphungu wa mtunduwu ku boma lake.

“A Nankhumwa adali nduna ya boma m’miyezi itatu yapitayo. Funso n’kumati n’chifukwa chiyani boma lawo silidaike ndondomekoyo m’dongosolo lawo la za chuma?” adatero Chakwera.

Mtsogoleriyo adanyogodolanso Nankhumwa posagwirizana ndi ganizo la boma lofuna kumangira aphungu onse nyumba zokhalamo m’madera omwe iwo amaimira, ati ponena kuti mkulu wosutsa bomayo samalabadira za mavuto omwe anthu a m’dziko muno amakumana nawo.

Koma Nankhumwa—pofuna kuphupha pa mtsutsowo—adayambitsa nkhani ina ya ndale yomwe idaoneka kuti ikhoza kugwedeza mtsogoleri wa dziko linoyo.

Iye adapempha Chakwera kuti auze nyumbayo mwachimvemvemve ngati mgwirizano wa Tonse Alliance—momwe chipani cha Malawi Congress Party (MCP) udagwirizana ndi zipani zina 8 kuphatikizapo cha UTM Party—uli ndi tsogolo.

“Mutiuzenso lero kuti kodi boma mukuyendetsali ndi la MCP kapena Tonse Alliance. Chifukwa tikudabwa kuti anthu ena omwe munkayenda nawo m’nyengo ya misonkhano yokopa anthu lero sakuonekanso. Kodi anthu ngati a Michael Usi, a Khumbo Kachale, ali kuti lero? Mwawataya kapena?” Adafunsa a Nankhumwa.

Koma poyankhapo, Chakwera adati palibe angaphwasule chimvano chomwe chili mu mgwirizano wa zipani za mu Tonse Alliance.

“Ndikumvetsetsa kuti ambiri akuyesa kusonkhezera kugawanika pakati pa ine ndi wachiwiri wanga komanso zipani zonse zomwe zili mumgwirizanowu. Koma sizitheka. Mgwirizanowu adachita kukonza yekha Yehova ndipo palibe angauthetse.

“Komanso ndinene kuti ambiri mwa omwe akutero—monga mkulu wotsutsa bomayu—sadavomereze kuti zinthu zidasintha ndipo Amalawi adawakana n’kusankha utsogoleri wodzipereka omwe wayambikawu. Zimenezi zangoonetseratu poyera kuti Malawi wa lero sangakhulupilirenso atsogoleri omwe sangadalirike pa utsogoleri wotumikira ngati wathuwu,” adatero Chakwera.

Mauwa adadzanso patangopita tsiku limodzi zipani za MCP ndi UTM Party zitatulutsa chikalata chotsimikiza anthu kuti mgwirizano wawo ulibe nthenya.

Chikalatacho chidalembedwa ndi Maurice Munthali komanso Joseph Chidanti Malunga, omwe ndi aneneri ku zipanizo.

Koma polankhulapo pa zochitika kadaulo pa zandale Mustafa Hussein adayamikira Chakwera poonetsa chidwi cholemekeza malamulo a dziko lino.

“Zayamba bwino komabe sizilephera, mpofunikabe kukonza pena ndi pena,” adatero katswiriyo.

Related Articles

Back to top button