Nkhani

Chakwera wakwera paphiri

Listen to this article

Akadaulo osiyanasiyana ati Pulezidenti Lazarus Chakwera waonetsa chamuna popita ku Nyumba ya Malamulo kukayankha mafunso a aphungu pankhani zokhudza dziko la Malawi.

Lachinayi, Chakwera limodzi ndi wachiwiri wake Saulos Chilima komanso nduna zina za boma adali ku Nyumba ya Malamulo komwe adayankha mafunso omwe aphungu makamaka a mbali yotsutsa adali nawo pa zomwe adalankhula potsegulira mkumano wa aphunguwo wokambirana za bajeti ya 2020 mpaka 2021.

Kadaulo pa zamalamulo Ernest Thindwa wati kupatula mayankho a nzeru omwe Chakwera adapereka m’nyumbayo, mtsogoleriyu wasonyeza kuti ndiwokonzekadi kutsata ndi kulemekeza malamulo aakulu a dziko lino.

“Lamulo limati Pulezidenti amayenera kukayankha mafunso pa Sitetimenti iliyonse yotsegulira mkumano wa bajeti ndiye kupita kokhako, waonetsa kuti ndi mtsogoleri otsata malamulo. Komanso tikasanthula momwe adayankhira mafunsowo, adayankha mwa nzeru kwabasi,” adatero Thindwa.

Koma iye adati n’zomvetsa chisoni kuti aphungu ena adataya mpata osowawo pofunsa mafunso opanda pake mmalo mofusa mafunso othandiza kukhuthalitsa Sona.

Naye kadaulo pa kayendetsedwe ka zinthu m’dziko Vincent Kondowe adati kukumana ndi aphungu maso ndi maso n’kuyankha mafunso awo kumasonyeza kuti mtsogoleri ndi wozindikira komanso ali pamwamba pa chilichonse chomwe akuchita.

“Kuyankha mafunso a aphungu maso ndi maso ndi njira yokhayo yomwe aphungu angaonetsetse kuti zinthu zikuchitika pambalanganda kuti aliyense azitha kutsatira. Chakwera waonetsa chitsanzo chenicheni cha demokalase,” adatero Kondowe.

Aka n’kachiwiri kuti Pulezidenti apite ku Nyumba ya Malamulo kukayankha mafunso a aphungu chiyambireni ulamuliro wa zipani zambiri. Bakili Muluzi adapitako kamodzi n’kuleka pomwe Bingu wa Mutharika, Joyce Banda ndi Peter Mutharika onse sadapiteko ku Nyumba ya Malamulo kukayankha mafunso.

Chakwera adayankha mafunso okhudza mbali zosiyanasiyana kuchokera mu Sona ndipo mfundo yake yaikulu adauza Nyumba ya Malamulo kuti aliyense akaika mtima pa malamulo ndi chilungamo, dziko la Malawi litukuka mosavuta.

Chakwera adayamba ndi kuyankha nkhawa za mtsogoleri wa mbali yotsutsa boma m’Nyumba ya Malamulo Kondwani Nankhumwa kenako nkhawa za aphungu payekhapayekha n’kumalizira mafunso ofunsidwa pompopompo.

Zina mwa nkhawa za Nankhumwa zidali ndalama za ukadziotche za aphunzitsi, zodya katatu patsiku, feteleza wa K4 495 pa thumba la makilogalamu 50, nyumba za aphungu, kusunthidwa kwa adindo ena ndi kumanga anthu pazifukwa za ndale.

Koma poyankha Chakwera adati Amalawi ali ndi chikhulupiliro m’boma la Tonse Alliance chifukwa akudziwa kuti likwanitsa zomwe lidalonjeza.

Iye adatinso kumanga nyumba za aphungu kuthandiza kupulumutsa ndalama za boma zomwe zimaonongeka polipira nyumba zobwereka zokhalamo aphunguwo.

“Boma la DPP lidaononga K2.7 biliyoni kulipira nyumba za aphungu muulamuliro wake. Ndalama zimenezi zikadapulumuka pakadakhala nyumba zokhalamo aphungu za boma,” adatero Chakwera.

Pa ndalama za ukadziotche, Chakwera adati Nankhumwa adali nduna miyezi itatu yapitayo ndipo sadaonetse chidwi choika ndalama za ukadziotche za aphunzitsi.

Aphungu osiyanasiyana adafunsa mafunso akukhosi kwawo koma funso lina lalikulu lidachokera kwa phungu wa ku Machinga Likwenu Bright Msaka yemwe adafunsa Chakwera kuti ngati akulemekeza malamulo abwezeretsa alembi omwe adawasuntha?

Chakwera adati palibe chifukwa chowabwezeretsera chifukwa sadalakwiridwe malingana ndi momwe zimakhalira m’boma lililonse kuti ogwira ntchito za boma amatha kusunthidwa bola ngati sadatsike udindo komanso malipiro ndi zolowa zina zili chimodzimodzi.

Mtsogoleriyu adadzudzula maganizo oti akusuntha alembi otsatira chipani cha DPP ponena kuti ngati alembiwo alidi a DPP, sakuyenera kugwira ntchitoyo chifukwa akupanga ndale mosemphana ndi malamulo.

Adatinso anthu asiye kukhulupirira kuti boma likumanga otsatira chipani cha DPP chifukwa akumanga ndi apolisi komanso apolisiwo akumanga anthu omwe amagwira ntchito m’boma ndipo adasokoneza osati a DPP.

Thindwa adati momwe wayambiramu, Chakwera asabwerere mmbuyo koma apitirize kutsatira zomwe lamulo limanena ndipo azipita ku Nyumba ya Malamulo kukayankha mafunso pakakhala kufunika kotero.

Related Articles

Back to top button