Chichewa

Chakwera wakwera

Listen to this article

Pamene Amalawi amayembekezera bungwe lachisankho kuti lilengeze zotsatira za chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino chimene chidachitika Lachiwiri pa 23 June 2020, zikuoneka kuti Lazarus Chakwera wa Malawi Congress Party (MCP) wapakira kale take, ndipo ulendo wa ku Nyumba ya Boma wapsa.

Chakwera adaima pamodzi ndi mtsogoleri wa UTM Party Saulos Chilima mumgwirizano wa zipani 9 pomwe amapikisana ndi yemwe amaimira mgwirizano wa zipani za Democratic Progressive Party (DPP) Peter Mutharika ndi womutsatira wake Atupele Muluzi wa United Democratic Front (UDF).

Mawu a mkazi wa malemu Bingu wa Mutharika, Calista oti ‘mlamu sangawine’ amene adalankhula mu 2019 akuoneka ngati aphera mphongo pamene Peter akusamuka kunyumba ya boma.

Zake zikuoneka zayera: Chakwera

Zotsatira zosatsimikizika kuchokera m’maboma onse zimaonetsa Chakwera adadya bwino m’chigawo cha pakati komwe adakokolola mavoti 1 615 959 kuliza Mutharika amene adapeza mavoti 190 994 ndipo Peter Kuwani wa Mbakuwaku Movement for Development (MMD) adapezako 9 765.

Chigawo chakummwera, Mutharika ndiye amatsogola ndi mavoti 1 471 010 kutsatidwa ndi Chakwera amene adapeza 375 247 ndipo Kuwani adali ndi 14 881.

Kumpoto, Chakwera adasinkha mavoti ambiri, 500 966 kutsatidwa ndi Mutharika amene adapeza 69 874 ndipo Kuwani adapeza 6 595.

Kuphatikiza zotsatirazi, Chakwera ndiye amaimba olileolile pamene amatsogola ndi 2 492 172. Mutharika amakwawa ndi 1 731 878 pamene Kuwani adali ndi 31 241.

Pofika dzulo, MEC idali itawerengetsera mavoti ochokera m’maboma 9 mwa 28 a dziko lino.

Mkulu wa bungwelo, Chifundo Kachale, usiku wa Lachinayi adati akuyesetsa kuti apereke zotsatira lero lisanadutse.

“Tikufuna kumaliza zonse pasanathe maola a pakati pa 36 ndi 48. Tili pantchito younikiranso bwino zotsatira zimene talandira kuchokera kumakhonsolo. Malamulo amatipatsa mphamvu younguza izi ndi kupereka zotsatirazo pakutha masiku osaposa 8,” adatero Kachale.

Chakummawa dzulo, Kachale adali atalengeza maboma 6 ndipo adanenetsa kuti pamene akubweranso adzalengeza zonse zomwe zionetse amene wapambana.

Chisankhochi chimachitika kutsatira mfundo ya bwalo la apilo mu May yomwe idatemetsa nkhwangwa pamwala kuti chisankhochi chichitike.

Padakali pano mtsogoleri wakale wa dziko lino Bakili Muluzi wapempha Amalawi kuti asunge bata pamene aliyense akudikira kumva zotsatira.

“Tikuyenera tilikonde dzikoli pogwirizana ndi zotsatira zomwe bungwe la MEC litulutse,” adatero Muluzi polankhula ndi wailesi ya Zodiak.

Related Articles

Back to top button