Nkhani

Chalaka Kinnah Tom sangatole

Aganyu tidagwiritsidwa utsi titalonjezedwa ndi yemwe anali mphunzitsi wa Flames Tom Santfiet kuti Flames ikavulaza Nigeria. Nigeria idatiumbudza 2-0.

Iye adatulutsa Robin Ngalande poseweretsa Atusaye Nyondo yekha kutsogolo ngakhale timaluza. Kodi amatchinjiriza chiyani? Uyutu adali ndi kampeni.

Aganyu zikutiwawabe. Tom wapita atalephera kuchita chomwe chidamuchotsetsa ku Belgium.

Ngakhale tikumva kuwawa, Fam ikusangalala chifukwa tathera nambala 2 m’gulu lathu. Suzgo Nyirenda ndiye watero.

Koma Nyirenda adziwe kuti palibe chosangalalira chifukwa panambalayi sitilandira kanthu komanso sitipita kulikonse.

Aganyu tilikhwira Fam chifukwa zonsezi ndi iyo. Uncle Tom adawatenga kuti? Nanga mudadziwana naye bwanji? Mudatsimikizika bwanji kuti angatithandize?

Ku Zambia adagonja kwa Angola ndi Zimbabwe. Ku Botswana adakagonjanso 1-0. Nigeria ndi iyo idamukodzetsa akuwonayo. Chanzeru wachita ndikupha Rwanda timu yomwe ndi ananso kwa ife.

Tikuona kuti vuto ndi mtima woipa umene udabzalidwa mwa Fam pokhulupirira aphunzitsi akunja. Izi sizingatithandize, mmalo mwake mukuononga timu yathu.

Mwatenga Tom koma wachoka atabalalitsa Flames. Joseph Kamwendo, Simplex Nthala adawathamangitsa ku timuyi. Sitikufuna tiyambe kuliriranso Kinnah Phiri chifukwa adachotsedwa akumanga timu.

Related Articles

Back to top button