Chichewa

Chenjerani, 2017 tisatuwe ndi njala’

Listen to this article

 

Lero ndi tsiku lakutha kwa chaka cha 2016. Pomwe masiku athera kuchitseko ndipo chaka cha 2017 chili pamphuno, akadaulo ena a zaulimi ati alimi asagone m’chaka chikudzachi kuti mwina mavuto a njala amene akhala akupana Amalawi zaka ziwiri zapitazi asatisautsenso.

Yemwe anali mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a zaulimi la Civil Society Agriculture Network (CisaNet), Tamani Nkhono-Mvula adati mphamvu zili m’manja mwa alimi kuti chaka chikudzachi kusakhale njala.

Mu 2015, mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika adalengeza kuti dziko lino lili pangozi kaamba ka madzi osefukira amene adasautsa m’chakacho. Koma paulimi wa 2015-2016, mvula idadula msanga zimene zidachititsa kuti zokolola zitsike.

Anthu kumalo ogulira feteleza a Optichem mwezi watha

Njala yakhudza Amalawi 6.8 miliyoni chaka chino moti mabungwe, boma ndi ena akhala ali pakalikiliki kuthandiza Amalawi ndi chakudya.

Pomwe mvula chaka chino yadza ndi mkokomo, mantha ali chaka chikudzachi kuti mwina anthu aonanso m’dima ndi njala yomwe ingagwe.

Koma Nkhono-Mvula akuti mantha angathedi kuchuluka ngati alimi angaseweretse mvula yomwe ikugwayi.

“Tidauzidwa kale kuti chaka chino kuli La Nina ndipo mwaona nokha momwe mvula ikugwera m’madera onse a dziko lino. Sitikuyenera kuyiseweretsa. Aliyense abzale nthawi yabwino kuti ikamasiya, mbewu zikhale zili pena,” adatero Nkhono-Mvula.

Iye adati ndi bwinonso alimi abzale mbewu zosiyanasiyana kuti chimanga chikavuta adzaone populumukira.

“Ngati tili ndi La Nina, ndiye kuti tilandira mvula yambiri, mvula imeneyi tisangoyirekerera, tiyeni tibzale mbewu zina monga mpunga, chinangwa, mbatata ndi zina kuti madziwa atithandize,” adatero Nkhono-Mvula. Mkulu wa bungwe la Farmers Union of Malawi (FUM) Alfred Kapichira Banda wati chaka chikudzachi pali chiopsezo cha njala chifukwa boma silinaikepo mtima pantchito yogawa makuponi ogulira feteleza ndi mbewu zotsika mtengo.

“Tikunena pano, madera ena sanalandirebe makuponi. Ichi ndi chiyambi cha njala. Alimi ambiri abzala, chimanga chawo chakula kwambiri moti chikufunika feteleza koma n’zachisoni kuti feteleza wa makuponi sadafike.

“Achikhala boma lidachfulumira ndi ndondomeko ya feteleza, si bwezi tikudandaula ndipo bwezi tikunena molimbika kuti chaka chikubwerachi sitikhala ndi njala monga zidalili zaka zapitazi,” adatero Banda.

M’chaka chikuthachi, kudagwa dzombe limene lidachecheta mbewu zambiri komanso lidaika pachiopsezo Amalawi amene ankadya dzombe lophedwa ndi mankhwala amene adapoperedwa.

Nayo misika ya Admarc idatsegulidwa mochedwa m’chakachi ndipo chimanga chimnagulitsa mokwera kuposa kwa mavenda. Thumba lolemera ndi makilogalamu 50 limagulitsidwa pa mtengo wa K12 500. Izi sizidakomere Amalawi ndipo mapeto ake samapita kukagula chimangachi.

Misika yomwe tidayendera mumzinda wa Blantyre, matumba a chimanga amagunda kudenga ngakhale patha miyezi itatu chifikireni chimangacho. n

Related Articles

Back to top button
Translate »