Nkhani

Chenjerani ndi mvula ya chaka chino

Listen to this article

Nthambi yoona zanyengo yati mvula chaka chino ibwera yamphamvu moti anthu omwe amakhala m’madera momwe mumakonda kusefukira madzi achenjere ndi kukonzeka.

Chenjezoli labwera pomwe kwangotsala mwezi umodzi kuti nyengo ya mvula iyambe polingaliranso kuti mvula ya chaka chatha idaononga zinthu ndi kuzulaza anthu ena.

Malingana ndi kalata yomwe azanyengo atulutsa yolosera mvula, kuyambira mwezi wa October 2021 mpaka March 2022, madera ambiri alandira mvula yokwanira koma ena alandira yopyola muyeso.

“M’madera ena, makamaka momwe mumakonda kusefukira madzi, mvula igwa yamphamvu moti ayembekezere ngozi za madzi osefukira,” yatero kalata ya nthambiyo yosayinidwa ndi wamkulu wake a Joram Nkhokwe.

Nthambiyi imatulutsa ulosi wake sabata iliyonse pofuna kuunikira boma ndi Amalawi za momwe nyengo ikhalire kuti akonzekele moyenera ndi kupewa ngozi.

Mneneri wa nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi a Chipiliro Khamula ati nthambiyo ili kale chile kuthana ndi ngozizo.

“Pali zambiri zomwe tachita monga kukhazikitsa ndondomeko zopewera ngati dziko komanso maboma ndipo zikutsindika pothamangitsa thandizo kwa anthu okhudzidwa,” atero a Khamula.

Mchaka cha 2017 madzi osefukila atavuta ku Lilongwe komanso 2019 madziwo atavuta ku Salima, nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi idagwiritsa ntchito asikari a nkhondo kukapulumutsa anthu.

A Khamula ati chaka chino, nthambiyo yakambirana kale ndi asilikari kuti akhale chile kupangira kuti ngozi zamadzi zitayambika, adzathandizile kupulumutsa anthu.

Iwo adatinso ngozizo zitati zagwa maphunziro sadzasokonekera ndi anthu okhala m’sukulu chifukwa malo osungirako anthuwo adakhazikitsidwa kale m’maboma omwe madzi amavuta.

“Malo osungirako anthu adakhazikitsidwa kale ndipo tidaunika kale nkhani zikuluzikulu monga kapewedwe ka Covid-19 komanso kusunga ulemu wa anthuwo m’malowo,” adatero a Khamula.

Iwo ati mothandizana ndi nthambi zina zaboma, akonza kale mauthenga oti aphunzitse anthu zokhudza ngozi zogwa mwadzidzidzi kuti azitha kuona zizindikiro n’kuthawa.

 Potsatira malangizo oterewa, maanja oposa 1 000 adasamuka m’malo mosefukila madzi n’kupita kumtunda mdera la mfumu Kaisi m’boma la Chikwawa.

Mfumu Maseya wa mboma lomwero adati anthu a mbali imodzi yokha ya madera atatu ndiomwe amavutika ndi madzi osefukila ndiwo adasamuka pomwe m’madera ena awiriwo sadasamuke.

“Madera omwe amavutika ndi Belewu, Kamisili ndi Kalima koma a kwa Kalima okha ndiwo adasamuka kupita kumtunda komwe madzi osefukila savuta,” adatero a Maseya

Iwo adati nthawi zambiri kukati madzi asefukira, madzi amayamba kudzadza m’mitsinje mvula isadagwe n’komwe mderalo.

“Madzi ambiri omwe amavuta kuno amachokera ku Mwanza ndiye tikaona kuti mtsinje wa Mwanza ukudzadza koma mvula isadagwe kwathu kuno, timadziwa kuti chaka chimenecho tivutika ndiye timachenjeza anthu,” adatero a Maseya.

Related Articles

Back to top button