Nkhani

Chenjezo: Makolo a ana opemphetsa azinjatidwa

Apolisi mumzinda wa Blantyre ati nthawi yatha ndipo tsopano ayamba kumanga makolo a ana amene apezeke akuyendayenda n’kumapemphetsa m’misewu ya mzindawu.

Mkulu woyang’anira mgwirizano wa apolisi ndi anthu papolisi ya Blantyre, Horace Chabuka, adanena izi masiku apitawa pasukulu ya Mbayani pomwe apolisi ndi bungwe loona za ufulu wa ana la Chisomo Children’s Club amalangiza makolo zomwe malamulo amanena pankhaniyi.street-kids

“Takhala tikulekerera izi kwa nthawi yaitali koma tsopano lamulo ligwira ntchito. N’zachisoni kuti ambiri mwa ana opemphetsa mumzinda wa Blantyre amachokera kuno ku Mbayani. Izi zikuchitika chifukwa ena amatumidwa ndi makolo awo kukapemphetsa komanso makolo ena salabadira za ana awo.

“Tsiku lina apolisi tidalowa m’chipinda choonetsera filimu 2 koloko mbandakucha ndipo ambiri adali ana kwambiri,” adatero Chabuka.

Iye adati ana opemphetsa ena amagwiritsidwa ntchito ndi achifwamba komanso akadzakula amakhala mbanda basi chifukwa sukulu imawalaka.

Malinga ndi mkulu wa Chisomo Children’s Club mumzinda wa Blantyre, Auspicious Ndamuwa, gawo lachitatu la malamulo otetezera ana limanenetsa kuti ndi udindo wa kholo lililonse kusamalira ana ake. Iye adati ndi udindo wa kholo kupatsa ana zakudya, zovala, pogona komanso kuonetsetsa kuti sakuchitiridwa nkhanza kapena kuponderezedwa kulikonse.

Malinga ndi iye, Lachiwiri likudzali ndi tsiku lokumbukira ana opezeka m’misewu ndipo, mogwirizana ndi mabungwe a Samaritan Trust komanso Step Kids Awareness (Steka), akonza zochitika mumzinda wa Blantyre zomwe mwa zina adzalangize anthu mumzindawu za lamulo lokhudza ana opemphetsa.

Izi zili apo, m’sabatayi nduna yoona za kuti pasakhale kusiyana pantchito pakati pa abambo ndi amayi, Patricia Kaliati adakana pempho la opemphetsa ena amene amati kuletsa anthu kuwathandiza kwachititsa kuti mavuto awo akule. Malinga ndi opemphetsawo, pomwe boma lidaletsa anthu kuthandiza opemphetsa, zawo zinada ndipo adapempha kuti boma liziwapatsa K50 000 pamwezi.

Koma Kaliati adakana pempholo, nati: “N’zosatheka zimenezo.”

Related Articles

Back to top button