Nkhani

‘Chidodo pamilandu’

Listen to this article

Mitima ya Amalawi yayamba kuwira ndi chidodo chomwe chikuchitika pa milandu ina yomwe akadaulo akuti ndi mlingo omwe Amalawiwo akugwiritsa ntchito kuti aone ngati boma la Tonse Alliance likwanitse malonjezo ake.

Milandu yomwe Amalawi akufunitsitsa kuona mapeto ake ndi yokhudza katangale, kuba chuma cha boma, kugwiritsa ntchito mphamvu za ofesi molakwika komanso zokhudza kupha ndi kusowetsa anthu achialubino.

Adamangidwa pa milandu ingapo: Chisale

Kadaulo pa kayendetsedwe ka zinthu Makhumbo Munthali wati yambiri mwa milanduyi imakwawa pakalowa ndale koma wachenjeza kuti anthu akazindikira kuti pali tsankho pa kayendetsedwe ka milandu, amayamba kuukira.

Iye wati mankhwala aakulu oluzanitsa anthu m’dziko n’kukwaniritsa malonjezo chifukwa anthuwo pokasankha atsogoleri amaunika mfundo ndi malonjezo n’kuona zomwe zikuwakomera.

Munthali adatinso boma likamayenda m’chilungamo ndi choonadi anthu amalolera kudzipereka pa chitukuko cha dzikolo.

Mlembi wamkulu wa mpingo wa CCAP wa Livingstonia Synod mlembi Levi Nyondo yemwenso amalankhula pa momwe zinthu zikuyendera m’dziko wati anthu ndi wokondwa kuti boma la mgwirizanowu lidayambapo kumanga anthu omwe akuwaganizira kuti adaba chuma cha boma koma wati chikondwererocho chikhoza kusanduka mkwiyo ngati milanduyo siyioneka tsogolo lake.

“Chomwe anthu akufuna ndi kuti ndalama zawo zomwe zidabedwa zibwerere ndiye popanda milandu kuyenda, ndalamazo sizingabwerere ndiye boma lionepo bwino pamenepo,” adatero Nyondo.

Panyengo ya kampeni, mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera ndi wachiwiri wake Saulos Chilima ankalonjeza kuti akadzangotenga boma adzathana ndi katangale poonetsetsa kuti milandu ya katangale yathamanga, milandu ya kuphedwa ndi kusowa kwa anthu achialubino idzayamba kuyenda komanso kuonetsetsa kuti ndalama zomwe zidabedwa m’boma zabwezedwa.

Ena mwa amene amangidwa m’boma la Tonse Alliance utalowa ndi Norman Chisale yemwe adali woteteza mstogoleri wa kale wa dziko lino Peter Mutharika; mneneri wa chipani cha UDF Ken Ndanga, yemwe anali mkulu wa bungwe la zamafuta la Malawi Energy Regulatory Authority (Mera) Collins Magalasi komanso mayi wa bizinesi Dorothy Shonga.

Boma lidamanganso apolisi ena kaamba kokhudzidwa ndi imfa ya Buleya Lule yemwe adali m’manja mwa apolisi pomwe bwalo limamva nkhani yomuganizira kuti adapha mwana wina wa chialubino.

Bungwe lomenyera anthu ufulu wa Human Rights Defenders of Coalition (HRDC) ndiwo udakoleza moto utalembera kalata ofesi ya mkulu oyendetsa za milandu ya boma kuti ofesiyo ifotokoze bwino chomwe milandu ya katangale, kuba chuma cha boma komanso ina siyikuoneka tsogolo lake.

Wothandizira Chakwera Sean Kampondeni adavomereza Lolemba pamsonkhano wa atolankhani ku Lilongwe kuti milandu ina sikusuntha ngakhale mkulu wa bungwe lolimbana ndi katangale la Anti-Corruption Bureau (ACB) Reyneck Matemba adati milandu yonse ikuyenda.

Matemba adati bungwe la ACB silingamanene chilichonse chomwe lapeza kapena likufufuza poopa kusokoneza kafukufuku wake koma pa nthawi yoyenera, bungwelo lidzatambasula zonse.

Iye adati pali milandu yambiri yomwe idayamba kuyenda litangosintha boma potsatira chisankho chachibwereza cha Pulezidenti chomwe chidachitika pa June 23 2020.

“Mwina HRDC ikunena milandu ina chifukwa milandu yomwe ili m’manja mwathu ikuyenda ndipo ina idalowa kale kukhoti kungoti milandu yambiri ndi yofunika kusamala polankhula kuti kafukufuku wake asasokonekere,” adatero Matemba.

Koma mkulu wa HRDC Gift Trapence adati bungwelo silidalandire yankho logwira mtima kuchokera kuofesi yoyendetsa milandu ya boma ya Director of Public Prosecutions (DPP).

“Sitikufuna ikhale nkhani yolozana zala koma tikungokumbutsa kuti adatilonjeza kuti milandu yomwe takhala tikugogodela kuti iziyenda adzayiyendetsa. Maso athutu ali pamenepo chitukwa akakwaniritsa zimenezi ife tidziwa kuti ankalonjeza zowona,” adatero Trapence.

Mtsogoleri wa bungwe lowona zachitukuko cha demokalase ndi chuma la Centre for Democracy and Economic Development Initiative (Cdedi) Silvester Namiwa wati boma lisapupulume poyankha koma limvetsetse nkhawa za Amalawi ndi kupereka chithunzithunzi choyenera.

“Iyi si nkhani yongoyankhapo poti yafunsidwa chifukwa mayankho omwe akuperekedwa pano adzakhala mafunso a mawa. Amalawi akufuna zinthu zooneka osati zolengeza chabe chifukwa mitima yawo idzapola akadzaona zomwe akuyembekezera,” adatero Namiwa. 

Related Articles

Back to top button
Translate »