Chichewa

‘Chidwi pantchito ya uphunzitsi chizilala’

Listen to this article

Bungwe la aphunzitsi m’dziko muno la Teachers Union of Malawi (TUM) lati zomwe lachita boma pokhazikitsa mfundo yoti ofuna kuphunzira ntchito ya uphunzitsi m’makoleji a boma (Teachers Training College—TTC) ayambe kulipira zichititsa kuti ambiri asakhale ndi chidwi cholowa uphunzitsi.

Woyendetsa ntchito za bungweli, Charles Kumchenga, adanena izi pothirirapo ndemanga pa ganizo la boma loti ophunzira ntchito ya uphunzitsi m’makoleji 8 a boma azilipira ndalama zokwana K105 000 pachaka kuonjezera pa ndalama zomwe boma limapereka.Teacher_teaching

“Pakalipano ngakhale mwana wapulayimale kumufunsa ntchito yomwe amafuna kudzagwira, ambiri satchula ya uphunzitsi chifukwa amaona okha mmene aphunzitsi akuvutikira, ndiye pano akuti munthu uzilipiranso ndalama zambirimbiri kuti ukhale mphunzitsi…ambiri chidwi sakhalanso nacho,” adatero Kumchenga pouza Tamvani.

Kumchenga adati zinthu zambiri sizili bwino n’kale m’makoleji a aphunzitsizi ndipo nthawi zonse boma limathamangira kuti ndalama ndizo zavuta likafunsidwa kukonza zina mwa zinthuzo.

“Ndi zoonadi boma lati aphunzitsi azilipira kuti aphunzire ntchito koma nkhawa yathu ili pakuti kodi izi zisintha zinthu m’sukulu zophunzitsiramo aphunzitsizi? Pali zambiri zofunika kukonza monga malo ogona, chakudya ngakhalenso malo ophunziriramo,” adatero Kumchenga.

Iye adati ndi zomvetsa chisoni kuti ntchito ya uphunzitsi imatengedwa ngati yotsalira kwambiri pomwe ndiyo gwero la ntchito ina iliyonse.

Kumchenga adatchulapo kusowa kwa nyumba zokhalamo aphunzitsi, kuchedwa kukwezedwa pantchito, malipiro ochepa, kuchedwa kwa malipiro ndi ndalama yolimbikitsira aphunzitsi akumidzi ngati ena mwa mavuto omwe amalowetsa pansi ntchito za maphunziro.

Koma poikira kumbuyo zomwe boma lachita, mlembi wamkulu muunduna wa zamaphunziro, Lonely Magreta, wati boma lidaganiza zoyambitsa kulipira m’ma TTC ndi m’sukulu zina pofuna kutukula ntchito za maphunziro.

Iye adati kudalira boma lokha sikungapindule kanthu chifukwa lili ndi zambiri zofunika kuchita ndiye kugawana udindo kungathandize kuti zinthu zisinthe msanga.

“Cholinga chathu n’chakuti ntchito za maphunziro zipite patsogolo. Mwa zina, tikufunitsitsa kuti zipangizo zophunzitsira ndi zophunzirira zizikhala zokwanira kuti wophunzira aliyense azikhala ndi buku lakelake panthawi yophunzira,” adatero Magreta.

Iye adati wophunzira aliyense ku TTC azipereka K105 000 pachaka yomwe ikuyimirira K20 pa K100 iliyonse yomwe imafunika kusula mphunzitsi mmodzi pachaka, kutanthauza kuti boma limafunika ndalama zokwana K525 000 pa mphunzitsi mmodzi.

Kupatula kuyambitsa zolipira m’ma TTC, boma latinso aliyense wofuna kukachita maphunziro ku Domasi komwe aphunzitsi amakaonjezera maphunziro awo, azilipira yekha. Wadipuloma azilipira K180 000 ndipo wofuna digiri ndi K280 000 pachaka

Kusinthaku kwakhudzanso sukulu za sekondale komwe fizi yakwera kufika pa K12 000 ku MCDE; K10 000 kusekondale yoyendera; m’sekondale zothandizidwa ndi boma K75 000. Kuyunivesite komwe akuti aliyense azilipira payekha, fizi ndi K275 000 pachaka, pomwe mmbuyomu osankhidwira kumakoleji a University of Malawi ankalipira K55 000 yokha pachaka, pamene ofuna kudzilipilira ankalipira K275 000.

Kuphatikiza apa, boma lati lasiya kupereka alawansi yomwe ophunzira ankalandira kuti iziwathandiza pogulira zipangizo monga mabulu ndi zowathandiza pamaphunziro awo.

Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe oyang’anira zamaphunziro m’dziko muno la Civil Society Education Coalition (Csec), Benedicto Kondowe, waati ganizo la bomali lili bwino, koma labwera molakwika.

Pocheza ndi Tamvani, Lachiwiri lapitali, Kondowe adati zomwe lachita boma polengeza kusinthaku modzidzimutsa zichititsa kuti anthu ambiri omwe adali ndi chilakolako cha sukulu alephere kuchita maphunziro awo chifukwa sadakonzekere mokwanira.

“Mwachitsanzo, mukatengera ndalama zomwe amalandira aphunzitsi, [wa PT4 wongoyamba kumene ntchito amalandira K54] ndi angati angakwanitse kusunga ndalama yokalipira ku Domasi kuti akaonjezere maphunziro? Izi zikutanthauza kuti aphunzitsi ambiri aimira pomwe alipo basi, ndiye maphunziro sangatukuke choncho,”adatero Kondowe.

Iye adati boma limafunikira kukonza ndondomekoyi ndi kulengeza panthawi yabwino kuti anthu akonzekere, osati kungowadzidzimutsa, ayi.

Related Articles

Back to top button