Chichewa

Chidyaabusa: Nthumbwana yofewetsetsa

Listen to this article

Zamkati mwa nyama monga ng’ombe kapena mbuzi zija ena amati nthumbwana ndi ndiwo zofewa zomwe ambiri amakonda kupatsa mafumu kapena akuluakulu pakakhala mwambo wa zochitikachitika. Nthumbwanazi zimakhala ziwalo zosiyanasiyana za mkatimo ndipo pakati pa izo pamakhala chiwalo china chomwe anthu amakhulupirira kuti oyenera kudya ndi abusa oweta ziweto. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Vincent Kalimba zokhudza chiwalochi.

Kalimba kufotokoza za mwambo wa chidyaabusa
Kalimba kufotokoza za mwambo wa chidyaabusa

Ndikudziweni…

Ndine Vincent Kalimba wa kwa Mbwatalika. Ndili pabanja ndipo ndimachita ulimi wa mbewu ndi ziweto.

 

Kodi kuno zolembana ntchito ya ubusa ziliko?

Kwabasi ndipo anthu ambiri omwe ali ndi ziweto ali ndi antchito osamala ziwetozo. Pena zimatheka watchito mmodzi kumasamala ziweto za anthu angapo bola ngati akukwanitsa kulongosola pokazilowetsa m’khola madzulo zikakhuta.

 

Ndikhulupilira nthumbawana mumazidziwa, kodi ndi chiyani?

Nthumbwana ndi zamkati mwa nyama monga ng’ombe kapena mbuzi. Zimakhala zofewa kwambiri bola zikaphikidwa bwino ndipo nthawi zambiri amadya ndi mafumu kapena akuluakulu pakakhala mwambo.

 

Zimakhala ziwalo zanji?

Ndi ziwalo zosiyanasiyana monga mtima, matumbo, mafuta, chifu, mphafa, chiwindi, kapamba ndi mapapo.

 

Ndiye pazomwe mwatchulazo amati palinso chidyaabusa, chimenechi chimaoneka motani?

Chimakhala ngati chija ena amati chibulangete kapena bafathaulo koma chimasiyana chifu poti chidyaabusa chimakhala chofewa kwambiri moti nthawi zina amatha kudya chachiwisi.

 

Zidatani kuti chikhale chidyaabusa?

Ndi dzina lomwe makolo kalelo adapereka potengera kuti eni ziweto akapha mbusa amamupatsa nthumbwana imeneyo kuti akadye. Mchitidwewu udazolowereka moti olo mwini ziweto aphe zingapo, mbusa amatenga nthumbwana zimenezozo.

 

Malipiro ake amakhala chidyaabusacho basi?

Ayi, amatha kumpatsanso nyama ina monga momwe mwini wakeyo waonera koma samalephera kumupatsa chidyaabusacho.

 

Nanga poti ena amati nthumbwana zimayenera kuperekedwa kwa mafumu kapena alendo ngati ulemu?

N’zoona, koma chidyaabusacho amatenga ndi osamala ziweto. Mafumu ndi alendo amawapatsa nthumbwana zinazo. N’zosachitanso kubisalira poti olo mafumu amadziwa kale mwambo umenewu.

 

Padalibe tanthauzo lapadera lochitira izi?

Padalibe kungoti kumakhala ngati kumulemekeza wosamalayo komanso zimamupangitsa kulimbikira pantchito yakeyo. Abusa ena amatha kunyanyala ngati chiweto chaphedwa koma osaona chidyaabusa.

 

Kunyanyala kwake kumakhala kotani?

Pena umatha kudabwa kuti dzuwa lakwera koma khola likadali lotseka. Kufufuza umangomva kuti mbusa wako watsegulira makola ena n’kudupha lakolo ndiye umangodziwa kuti akulonjerera chidyaabusa cha chiweto chomwe udapha.

 

Ndiye kukambirana kwake kumakhala kotani?

Kukambirana basi monga anthu. Mwina kungopepesana ndi mawu ngati mumamvana kapena kumpatsa mazira a nkhuku kapena ndalama kuti apitirize ntchitoyo.

 

Limakhala pangano polembana ntchitoyo?

Ayi ndithu, koma kuti zidangokhala ngati mwambo wake kuti mbusayo azilandira nthumbwana imeneyo ndipo ambiri amangootcha n’kudya osatinso kudikira zokaphika kunyumba.

 

Bwanji mabwanawo samangomusiya wonyanyalayo n’kulemba wina?

Ziweto n’zovuta kwambiri, makamaka ng’ombe ndi mbuzizo. Ena amakhulupirira kuti khola limatengera mutu wa mbusa ndiye kusinthasintha abusa nthawi zina kumasokoneza mphumi. Komanso pali ng’ombe zina zomwe zimazolowera mbusa wawo moti akasintha zimakhoza kuchita ukali. N’chifukwa pena mumaona kuti mbusa watsegula khola koma ng’ombe zina sizikutuluka.

 

Masiku ano za chidyaabusa zikadalipo?

Zilipo m’madera ena koma mwambiri zidazimirira n’kutsukuluzika kwa chikhalidweku komanso kusakanikirana kwa mitundu ndiye pang’onopang’ono zina zidazilala. n

Related Articles

Back to top button
Translate »