Chichewa

Chilango cha kunyonga chiutsa mapiri pachigwa

Listen to this article

 

Ndawala yofuna kubwezeretsa chilango choti wopha mnzake naye aphedwe yavumbulutsa maganizo osiyanasiyana pakati pa mafumu, anthu ndi boma.

Ndawalayi idachitika Lachinayi lapitali mumzinda wa Lilongwe pomwe phungu wa kummwera kwa boma la Mulanje Bon Kalindo adatsogolera khamu la anthu kukapereka chikalata ku Nyumba ya Malamulo chopempha kuti chilangochi chibwerere.

Kumayambiriro a sabata yathayi, ndawalayi isadachitike, nduna ya zofalitsa nkhani Patricia Kaliati idanenetsa kuti boma lilibe maganizo obwezeretsa chilangochi potengera pangano la maiko onse.

Kaumba akaseweza moyo wake  wonse kundende
Kaumba akaseweza moyo wake
wonse kundende

“Dziko la Malawi lidasayina nawo mapangano ambirimbiri okhudza za ufulu wa anthu ndiye sitingabwerere mmbuyo n’kuyamba kuphwanya pangano lomwe tidasayina tokha,” adatero Kaliati polankhula ndi atolankhani ku Nyumba ya Malamulo.

Koma mafumu ena akuluakulu monga Chindi wa ku Mzimba m’chigawo cha kumpoto ndi Kabudula wa chigawo cha pakati adati iwo akuona kuti munthu wopha mnzake akuyenera nayenso aphedwe, osanyengerera.

Chindi adati koma mpofunika kulingalira mofatsa pogamula milandu yotereyi kuti chilungamo chioneke kuti kodi adapha mwangozi kapena dala kuti zilangozo ziperekedwe.

“Kupha kuli pawiri-mwadala ndi mwangozi. Apapa tikhazikike pa wopha mwadala monga momwe opha maalubino amachitira. Amenewa akuyenera kuphedwa basi, osawanyengerera, ayi, chifukwa nawonso sadanyengerere mnzawoyo,” adatero Chindi.

Naye Kabudula adati palibe njira ina yoposa kupha anthu otere chifukwa moyo wawo uli ngati zilombo zolusa zomwe zingaononge mtundu.

Onsewa adasemphana ndi mfumu Chapananga ya ku Chikwawa m’chigawo cha kummwera yomwe idati chilango chakupha si chilango chabwino, bola ndende moyo onse.

“Kwa ine zakuphazo ayi, bola atati opha mnzake azikakhala kundende moyo wake wonse basi,” adatero Chapananga.

Anthu osiyanasiyana omwe adacheza ndi Msangulutso adaperekaso maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya chilangochi.

Bernadette Kaonga, wa ku Area 49 mumzinda wa Lilongwe, adati iye sangavomereze kuti anthu aziphedwa. Iye adati njira yabwino n’kupeza njira yoti zophanazo zitheretu kapena, apo ayi, kundende moyo wonse.

Mnzake yemwe adali naye limodzi panthawiyo, Mary Molosi, adati iye akuganiza kuti njira yomwe ingathetse zophanazo ndi chilango chophedwa, basi.

Pa 14 June, 2016, Samson Kaumba wa zaka 33, adakhala munthu oyambirira kupatsidwa chilango chokakhala kundende moyo wake wonse pamlandu wokhudzana ndi nkhanza kwa alubino kubwalo lalikulu la milandu la Mzuzu. n

Related Articles

Back to top button
Translate »