Chichewa

Chilango chowawa kwa wogulitsa nyama ya galu

Listen to this article

 

Bwalo la majisitireti la Balaka lapereka chilango chowawitsa kwa mkulu amene wakhala akugulitsa nyama yagalu kwa zaka 14.

Pamene gawo 181 la zilango m’dziko muno, limene apolisi adamangira Ishmael Jumbe, limati wolakwira lamulolo akhale kundende miyezi itatu kapena kulipira chindapusa cha K50, wogamula Victor Sibu adati mkuluyo akakhale kundende chaka chimodzi.

Malinga ndi mneneri wa polisi ya Balaka Joseph Chadwala, woweruzayo sadapereke mwayi woti Jumbe n’kupereka chindapusa.

“Asanagamule, Jumbe adapempha bwalolo kuti limupatse chilango chocheperako chifukwa anthu amene adawadyetsa nyamayo adamukhululukira kale. Iye adatinso ali ndi ana atatu amene amadalira iye,” adatero Chadwala.

Jumbe: Galu amakoma ngati nyama yambuzi
Jumbe: Galu amakoma ngati nyama yambuzi

Koma Sibu adati chifukwa adaonetsa kuti ili ndi khalidwe lake kugulitsa nyama yagalu pempho lake silidamveke.

Polankhula ndi Msangulutso ali m’manja mwa apolisi Lachitatu lapitali, Jumbe adati wakhala akugulitsa nyama yagalu kwa zaka 14 ndipo adaiyamba mumzinda wa Blantyre ku Mbayani pomwe amakazinga nyamayo pamalo otchedwa Chiimirire.

Jumbe, yemwe ndi wa m’mudzi mwa Kangaude kwa T/A Nkaya m’boma la Balaka, adanjatidwa Lamulungu pa 15 November pamene makasitomala ake adamupeza akusenda galu.

“Pomwe ndinkayamba izi, ndidali ndi mnzanga, timagulitsira pa ‘Chiimirire’ komanso m’malo omwera mowa. Ndidali ndi makasitomala ambiri amene amakonda bayabaya,” adatero Jumbe, amene akuti ankakonda kugulitsa kanyenya wa nyama ya galuyo madzulo.

Iye adati mosakhalitsa mnzakeyo adamwalira, zomwe zidamuchititsa kuti apite ku Balaka komwenso adakapitiriza bizinesiyo.

“Sinditola agalu akufa, ndimachita kugula wamoyo n’kumupha ndekha. Galu amene andigwira nayeyu ndidagula pamtengo wa K1 000. Uyuyu ndiye ndidamuphera panjira chifukwa atandigulitsa, amavuta kuyenda. Ndidamupha ndi kumumangirira panjinga.

“Kunyumba ndimafika cha m’ma 12 koloko usiku ndipo ndidangofikira kumusenda. Mmawa ndidamuphika m’chidebe, kenako ulendo wakumsika wa Njerenje kukagulitsa,” adatero Jumbe.

Iye adati chomwe amataya akapha galu ndi mutu ndi mapazi komanso chikopa koma zam’mimba zonse amaphikira kumodzi.

“Mutu ndi zipalapasiro [mapazi] komanso chikopa ndi zomwe ndimachotsa. Zam’mimba ndi ziwalo zina timaphikira kumodzi. Uyuyu adali wofula ndiye adali wamafuta kwambiri moti chidebecho adachita kumata mafuta okhaokha,” adatero.

Titamufunsa ngati iye adayamba wadyapo galu, adati ndi nyama yabwino ndipo zikadakhala bwino nyamayi ailoleze kuti izigulitsidwa poyera.

“Momwe imamvekera nyama yambuzi ndi chimodzimodzi ndi nyama yagalu. Yofewa komanso yamafuta. Ena amati nyama ya galu imawawa koma n’zabodza, iyi ndi nyama yokoma ndipo ine ndidayamba kalekale kudya,” adatero Jumbe.

“Ndipo ikangofika pamsika simachedwa kutha, aliyense amafuna abaye basi. Ziwaya za anthu ena zimapezeka sizinathe koma ine chatha kale m’maola awiri okha.”

Iye adati atakagulitsa nyama ya galuyo, Loweruka mmawa kudalawirira anthu kunyumba kwake kukamufunsia za nyama yomwe adawadyetsayo.

“Iwo amati adamva mwana akunena kuti adandiona ndikusenda galu. Ndidakana powayankha kuti idali nyama ya mbuzi. Kenaka atavuta ndidawauza zoona ndipo adanditengera kwa mfumu. Mosakhalitsa ena adadziwitsa apolisi omwe adabwera kudzandimanga.

“Ndikungopempha kuti andikhululukire ndipo sindidzachitanso. Andimvetse chifukwa agalu amene ndimagula amakhala abwinobwino, bola akadakhala achiwewe bwezi ili nkhani ina,” adaonjeza.

Mmodzi mwa anthu amene adabaya nawo nyama yagaluyo koma sadafune kutchulidwa, adati sadazindikire kuti idali ya galu.

“Ndidalibe chidwi kuti ndimvetsere bwinobwino pamene ndimadya, basi ndidangoti ndi nyama yambuzi. Koma nditangomva zoti adali galu, ndidadziguguda ngati ndisanze komabe sizikadatheka,” adatero.

Anthu 7 amene adadya nawo nyamayo adawatumiza kuchipatala cha Balaka kuti akawaunike, koma onse awatulutsa, malinga ndi Chadwala.

Related Articles

Back to top button
Translate »