Nkhani

Chilima akhazikitsa UTM ku Blantyre

Listen to this article

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Saulos Chilima, mawa akhazikitsa gulu la United Transformation Movement (UTM) ku Njamba mu mzinda wa Blantyre.

Polankhula ndi Tamvani, mneneri wa gululi, Joseph Chidanti Malunga, adati chilichonse chokonzekera kukhazikitsidwaku chili mchimake.

Chilima kukhazikitsa UTM pa bwalo la Masintha ku Lilongwe

“Tili ndi masomphenya a aakulu omwe amangiririka pa ndondomeko 12 zosinthira dziko lino. Anthu aku Lilongwe alawa kale zina mwa zinthu zomwe tikufuna kuchita,” adatero Malunga.

Msonkhanowu udayenera kukachitikira pa bwalo la sukulu ya Nyambadwe, koma Malunga adati asintha kaamba koti bwalolo ndi laling’ono.

Wapampando wa gululi, Noel Masangwi, adati ukatha msonkhano wa ku Blantyre, akakhazikitsanso gululo m’chigawo cha kumpoto.

Sabata yatha UTM idakhazikitsidwa pa bwalo la Masintha mu mzinda wa Lilongwe ndi chinantindi cha anthu chidafika pamwambowo.

Ena mwa anthu omwe adafika ndi Sipika wa Nyumba ya Malamulo, Richard Msowoya, akazi a atsogoleri akale a dziko lino, Callista Mutharika ndi Patricia Shanil Dzimbiri, phungu wa m’boma la Balaka, Lucius Banda, aphungu a DPP a m’boma la Mulanje, Bon Kalindo ndi Patricia Kaliati.

UTM idayambika Callista atapempha mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, kuti apereke mwayi kwa Chilima kuti adzaimire DPP pa zisankho za chaka cha mawa.

Mutharika adakana pempholo zomwe zidachititsa kuti Chilima ndi anthu ena atuluke m’chipanicho n’kuyambitsa gulu la UTM.

Related Articles

Back to top button