Nkhani

‘Chilungamo cha pakati pa usiku ayi’

Listen to this article

Gulu la za maufulu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) lati nthambi yoona za makhoti komanso bungwe la oimira ena pamilandu la Malawi Law Society (MLS) aunike bwino chomwe chachitika kuti yemwe akumuganizira kuti adafuna kupereka chiphuphu kuti oweruza akometse chiweruzo, Thom Mpinganjira, atuluke m’chitokosi cha polisi pakati pausiku.

Bungwe lothana ndi katangale la Anti-Corruption Bureau (ACB) Lachitatu mmawa lidamanga Mpinganjira mmodzi mwa omwe akuganiziridwa kuti ankafuna kupereka ziphuphu kwa majaji omwe akuyembekezeka kugamula mlandu wachisankho cha Pulezidenti.

Matemba kulowa m’khoti Lachinayi

Bwalo la milandu, sabata ikuthayi lidalengeza kuti chigamulocho chiperekedwa pakati pa 27 January ndi 3 February.

Malingana ndi chikalata cha ACB, Mpinganjira amayembekezeka kukaonekera kukhoti Lachinayi komwe akadakhala ndi mwayi wopempha belo koma mkulu wa ACB Reyneck Matemba adati adadzidzimuka kumva kuti mkuluyo adatuluka m’chitokosi pakati pa usiku.

“Sindikumvetsa kuti zidayenda motani kuti mpaka anthu anyamuke wa ku Zomba nkukumana pakati pausiku popanda mbali imodzi kuimiriridwa n’kupatsana chilolezo chochotsa mphamvu zomangira munthu oganiziridwa,” adatero Matemba.

Mkuluyu yemwe amamvekadi kuti adayendedwa pansi, adati ACB ndi oimilira Mpinganjira zidamvana kuti nkhaniyo ipite kukhothi mmawa Lachinayi kuti Mpinganjirayo akapemphe belo komweko.

Pricipal Resident Magistrate Ben Chitsakamile wa ku Zomba ndiye

adapereka mphamvu zochotsa chilolezo chomangira Mpinganjira pakati pausiku ndipo HRDC yati apa mpoyenera kufufuzidwa bwino.

HRDC yati ikufuna Mpinganjira amangidwenso ndipo ndondomeko yoyenera yoyendetsera za milandu itsatidwe komanso onse omwe akukhudzidwa ndi nkhaniyi amangidwe mwachangu kuti chilungamo chioneke.

Apa, HRDC yati Amalawi agwira ntchito limodzi ndi ACB pofuna kuti chilungamo pankhani yofuna kugula majaji chioneke mpaka pothera pake.

Sabata yatha, HRDC idatsogolera Amalawi pachionetsero chokapereka kalata yodzudzula Matemba chifukwa chobisa maina a anthu omwe amaganiziridwawo ndipo adamupatsa maola 72 kuti akhale atatchula anthuwo.

Poona kuti maolawo akwana koma maina sadatchulidwe, HRDC idapangitsa msonkhano wa atolankhani komwe amakawauza kuti achita chionetsero china chofuna kuti Matemba atule pansi udindo koma pochoka apo, ACB idali itatulutsa kalata yolengeza kumangidwa kwa Mpinganjira.

Related Articles

Back to top button