Nkhani

Chimanga chikololedwa chochepa—Unduna

Listen to this article

Kauniuni woyamba wa zokolola wasonyeza kuti chaka chino Amalawi akolola chimanga chocheperako kusiyana ndi chaka chatha, chikalata chimene unduna wa malimidwe watulutsa chatero.

Chaka chilichonse undunawu umachita kauniuni katatu pa mbewu, ziweto ndi nsomba pofuna kuunikira kuti zokolola zikhala zotani.mcp

Kauniuni woyambayo wasonyeza kuti chaka chino mlingo wa chimanga utsika kuchoka pa matani 2 776 277 chaka chatha kufika pa 2 719 425, ndipo izi zikutanthauza kuti pa makilogalamu 100 alionse omwe tidapeza chaka chatha, chaka chino pazichoka makilogalamu awiri.

Kauniyu wapezanso kuti fodya wa chaka chino achuluka kuchoka pa makilogalamu 192 967 541 chaka chatha kufika pa makilogalamu 211 083 000 chaka chino pomwe thonje atsika ndi makilogalamu 43.2 pa makilogalamu 100 alionse omwe adakololedwa chaka chatha.

Undunawu wati mpunga uchuluka ndi makilogalamu 1.4 pa makilogalamu 100 omwe adakololedwa chaka chatha pomwe mtedza uchuluka ndi makilogalamu 4.5, nyemba 5.2 ndipo nandolo 3.1 pa makilogalamu 100 aliwonse omwe adakololedwa chaka chatha.

Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a zaulimi wa Civil Society Agriculture Network (Cisanet) Tamani Mvula Nkhono adati kauniuni wa mtunduwu ndiwofunika chifukwa umapereka chithunzithunzi cha kakololedwe.

Iye adati undunawu wachita bwino kutulutsa zotsatira zakauniuni woyambayu koma lipitirize kuunikanso kawiri kamene katsala.

Related Articles

Back to top button