Nkhani

Chipatala cha boma chitsekedwa loweruka

Listen to this article

Miyoyo ya anthu pafupifupi 50 000 ozungulira chipatala cha Mkanda Health Centre m’boma la Mchinji imaikidwa pachiopsezo Loweruka chifukwa sichitsekulidwa patsikulo mosemphana ndi dongosolo la unduna wa zaumoyo.

Mneneri wa unduna wa zaumoyo Adrian Chikumbe adauza Msangulutso  Lolemba kuti chipatalacho chimayenera kutsekulidwa ndi Loweruka lomwe—kuchoka m’mawa mpaka nthawi ya nkhomaliro. Kuposera apo, madotolo amayenera kusamala odwalika zedi kapena a matenda obwera mwadzidzidzi.

Ngakhale izi zili choncho, chipatalachi chimalandiranso odwala kuchokera m’zipatala zina zazing’onozing’ono 5, omwe akafika pamalopa Pachiweru, amakhala kakasi.

Kafukufuku wathu wasonyeza kuti chipatalachi sichimatsekulidwa Loweruka chifukwa mkulu woyang’anira pamalopa, yemwe sitimutchula dzina, amapemphera tsikulo.

Ndipo kusatsekulidwa kwa chipatalachi kukuchititsa ena mwa anthu ofuna thandizo kupita kuzipatala zomwe si zaboma kapenanso chipatala cha Tamanda chomwe chili m’dziko la Zambia.

Bambo wina, yemwe adakana kutchulidwa dzina, adati mwana wake wa zaka 12 amene adafika naye pachipatalapo kumapeto kwa 2015 adamwalira kaamba kosowa chisamaliro. Iye adati adapita ndi mwanayo akuonetsa zizindikiro za malungo Lachisanu nthawi itadutsa 11 koloko usiku koma dotolo adakana kuwathandiza usikuwo.

“Adakana kudzuka ndipo patadutsa maola awiri mwanayo adamwalira. Apa tidapempha mlonda kuti akawauze kuti mwanayo watisiya ndipo atithandize koma adangomuuza kuti tizipita kumudzi,” adatero bamboyo,

Wina mwa okhudzidwa ndi vutoli, yemwe ndi mphunzitsi pa sukulu ya sekondale m’deralo, adati wabwererapo kawiri konse m’chaka chathachi pachipatalachi.

“Ulendo wina, mwezi wa October, ndidabwerera ndi mwana wanga wa zaka zitatu yemwe amadwala mphumu. Chifuwachi chitakwera cha m’ma 7 koloko usiku wa Loweruka, ndidathamangira kuchipatala komwe ndidapezako anthu ena awiri odwala akudikirira,” adatero iye.

Iye adaonjeza kuti atabwera mkulu wa pachipatalapo, adawanyengerera kuti awathandize ndipo adangowalembera enawo kuti azipita chipatala cha kuboma.

“Koma mwana wanga adakanitsitsa kumulemba mpaka adatibweza,” adatero munthuyo yemwe wakana kutchulidwa dzina.

Iye adapita kuchipatala cholipira komwe adalipira K4 500.

Mkulu wa komiti ya kayendetsedwe ka chipatalacho ya health advisory committee (HAC) Thomas Bisiketi adatsimikiza kuti odwala saonedwa patsikulo ndipo mbali ya amayi obereka yokha ndi yomwe imakhala ikugwira ntchito.

“Mkulu wachipatalapo sagwira ntchito patsikuli, koma ife ngati a HAC timaoona ngati ndi momwe zipatala zonse zaboma satsegula Loweruka,” adatero Bisiketi.

Malinga ndi wapampando wa komiti ya chitukuko kwa m’derali  Anorld Chitedze, chipatalachi chakhala chisakutsekula Pachiweru kwa zaka zitatu tsopano.

Iye adati chipatalachi chili ndi ogwira ntchito asanu okha, omwe atatu aiwo ndi anamwino, ndipo awiri ndi olembera odwala.

“Mkulu wachipatalachi amatiyankha kuti amapita kutchalitchi Pachiweru ndipo chipatala satsekula. Koma ife timadabwa kuti bwanji sauza ena omutsata kuti azithandiza anthu patsikulo?” adatero iye.

Popheramphongo, Mfumu yaikulu Mkanda idati kafukufuku wake wasonyeza kuti chipatalachi sichitsekulidwa Pachiweru ndipo odwala ochokera m’zipatala zazing’ono zozungulira deralo monga Kazyozyo, Kaligwazanga ndi Gumba, amawapatsa bedi podikira Lolemba.

“Odwala akabwera Lachisanu, samawaona tsiku lomwelo. Iwowa  amapatsidwa bedi mpaka Lolemba. Sitikudziwa kuti nkutani. Chaka chatha tidapempha kuti atichotsere, koma tangodabwa kuti wagoneranso. Pano nzeru zatha,” idatero mfumuyo.

Iyo idati masiku ena mkuluyo amatha kungothandiza owadziwa kapena munthu akamkomera mtima.

Iye adati nkhaniyi idakafika ku likulu kwa bomalo ndipo adamkhazikako bwalo pamaso pa akuluakulu a boma ndi dotolo wamkulu wa bomalo yemwe pano adasamukira ku boma lina.

Poyankhako dotolo wa mkulu m’boma la Mchinji Juliana Kanyengambeta adati ndizokhumudwitsa

Related Articles

Back to top button
Translate »