Nkhani

Chipatala chidatha 2009, sichidatsegulidwebe

Listen to this article

Anthu ndi mafumu ku Ligowe kwa T/A Mlauli m’boma la Neno apempha boma kuti liwatsekulire chipatala chomwe chidatha mu 2009 koma mpaka lero sichinatsekulidwe.

Chipatalacho adachimanga  ndithandizo la European Union (EU) ndipo kusachitsegulira kwachititsa kuti anthu azipita kuchipatala cha Ligowe Health Centre chomwe chili ndi mabedi awiri okha koma chimathandiza anthu oposa 14 000.

Mafumu komanso anthu kumeneko ati atopa ndilonjezo laboma kuti adzatsekula chipatalacho kotero apempha kuti chipatalacho chitsekulidwe.

Anthu angapo amene tidacheza nawo, kuphatikizapo T/A Mlauli, adatsimikiza kuti akusowa mtengo wogwira ndipo akusaukira thandizo kaamba ka kusatsegula kwa chipatalacho

“Ena sakupitanso kuchipatalako pomwe ena akuyenda maulendo ataliatali kufuna chipatala, chikhalirecho chipatala tilinacho.Ndife okhudzidwa,” adatero Mlauli.

Iye adati phungu wa kumeneko, Reen Kachere wakhala akulonjeza kuti adzatsekula chipatalacho koma palibe chikuchitika.

Malinga ndi ogwira ntchito ena pachipatalapo, nthawi zina abambo ndi amayi akumagona chipinda chimodzi.

Chipatalacho chomwe chili ndichipinda chimodzi chothandizira odwala chilibe nyumba ya ogwira ntchito ndipo ogwira ntchitowo akukhalira kutali ndi chipatalacho.

Chipatalacho chilibe namwino ndipo chilibenso chipinda chothandizira amayi apakati koma mayi yemwe wavutika akuti amathandizidwa.

“Ndabereketsa amayi oposa 40.Koma zili ndimavuto ake chifukwa zipangizo zomwe timagwiritsa ntchito timayenera tiziphike tisadagwiritsire ntchito munthu wina koma zotere sizikuchitika zomwe zikupereka mantha opatsirana matenda,” adatero mkuluyu.

Mkulu wa bungwe loona za ufulu wa anthu pa zaumoyo la Malawi Health Equity Network (MHEN) Martha Kwataine wati pali zipatala zingapo zimene sizinatsegulidwe ngakhale zidatha kalekale.

Adapereka chitsanzo cha zipatala za  Misuku ndi Kapolo Health Centre ku Karonga komanso Malidade ku Mzimba.

“Mavuto onsewa angathe ngati boma litatsekula chipatala chatsopanocho.Unduna wazaumoyo ukuyenera kulowererapo ndipo chipatalacho chitsekulidwe posakhalitsa,” adatero Kwataine.

Mneneri wa boma muundunawu, Henry Chimbali wati tilankhule ndi District Health Officer (DHO) wa bomalo, Victor Nkhoma, adati nkhaniyo ili m’manja mwa bwanamkubwa wa bomalo, Macloud Kadam’manja.

Kadam’manja wati sabata ziwiri zathazi adakumana ndipo adalembera Nkhoma kuti pa 1 Novembala chaka chino chipatalacho chitsekulidwe.

Koma pomwe timasindikiza nkhaniyi n’kuti chisanatsekulidwe.

 

Related Articles

Back to top button