Nkhani

Chipatala chidzapulumutsa K730m pachaka

Listen to this article

Chipatala cha khansa chomwe boma likumanga ku Lilongwe chikatsegulidwa mwezi wa September chaka chino, boma kudzera ku Unduna wa Zaumoyo lizipulumutsa K730 miliyoni pa chaka.

Ndalamazi ndi zomwe boma limagwiritsa ntchito potumiza anthu odwala khansa kunja kukalandira thandizo lomwe tsopano lizipezeka m’dziko

momwemuno kudzera kuchipatalachi.

Mkulu wa bungwe loona zaumoyo la Malawi Health Equity Network (Mhen), George Jobe, wati iyi ndinkhani yabwino chifukwa Unduna wa Zaumoyo uzigwiritsa ntchito ndalamazi pa zinthu zina zofunikira monga kugula mankhwala ndi mafuta othira m’maambulasi.

“K730 miliyoni ndi ndalama zambiri zedi zoti kuzigwiritsa ntchito bwino zikhoza kupindulira anthu ambiri ku ntchito ya zaumoyo. Monga tikudziwa, mafuta a ambulansi ngakhalenso mankhwala zimasowa,” adatero Jobe.

Unduna wa zaumoyo wati chiwerengero cha anthu omwe ali ndi khansa chodziwika m’dziko muno ndi 15 000 ndipo boma limatumiza anthu 40 mwa anthuwa kunja kukalandira thandizo la mankhwala ndipo munthu mmodzi amafunika K22 miliyoni kuti apite kunja, akalandire thandizo n’kubwerako.

Bungwe loona za anthu odwala ndi khansa la Cancer Association of Malawi lati thandizo lomwe odwala khansa amalandira kuchipatala cha Gulupu ku Blantyre ndi loperewera ngakhale kuli mpumulo pang’ono.

Mkulu wa bungwelo, Regina Njirima adati khansa imafunika chipatala chakechake chifukwa anthu odwala khansa amafunika kuonedwa pafupipafupi komanso kuwasakaniza ndi anthu odwala matenda ena kumawapangitsa kudzimvera chisoni kwambiri.

“Wodwala khansa amakhala ndi nkhawa zambiri kotero amafunika pamalo oti nkhawazo zizichepa. Njira yabwino n’kukhala ndi chipatala chawochawo chomwe chili ndi zipangizo komanso akadaulo othandiza odwalawo” adatero Njirima.

Mmodzi mwa anthu omwe adadwalapo khansa ndipo adachira atapita kuchipatala Janet Bonwel a kwa T/A Ndindi ku Salima adati kupeza thandizo la khansa M’malawi n’kovuta moti anthu ambiri akuvutika ndi matendawa.

Iye wati adapezeka ndi khansa ya mmwendo mu 2001 ndipo kuzipatala zosiyanasiyana komwe amapita amangopatsidwa Panado yemwe samachotsa n’komwe ululu omwe adali nawo.

Iye wati adakapeza thandizo kuchipatala cha Ndimoyo ku Salima komweko.

“Ululu wa khansa siwamasewera. Ndidachita kusiya kugwira ntchito iliyonse ndipo sindimatha kugona chifukwa chaululu kumangobuula usiku ndi usana. Ndidalowera uku ndi uko koma osapeza thandizo mpaka ndidafika potaya mtima kuti ndizingodikira imfa,” adatero Bonwel.

Iye wati chipatala cha khansa chibweretsa mpumulo waukulu kwa anthu omwe ali ndi khansa.

Ntchito ili mkati kuchipatala cha khansa

Related Articles

Back to top button
Translate »