Chichewa

Chipatala chiutsa mapiri pachigwa

 

Akuluakulu ena a khonsolo ya Lilongwe ndi kontilakitala yemwe akumamanga chipatala cha Biwi mumzinda wa Lilongwe, ayankha mafunso zitadziwika kuti pantchitoyi pakukhala ngati padayenda zachinyengo.

Nduna ya maboma ang’onoang’ono Kondwani Nankhumwa wanenetsa kuti ena anjatidwa pankhaniyi kafukufuku akatha.

Chomwe chautsa mapiri pachigwa nchakuti chipatalacho chayamba kale kugwa mbali imodzi chisadathe komanso makoma ali ming’alu yokhayokha.

Nankhumwa (Kumanzere) sadakhulupirire kuona mmene ntchito ya  Chipatala cha Biwi ikuyendera
Nankhumwa (Kumanzere) sadakhulupirire kuona mmene ntchito ya
Chipatala cha Biwi ikuyendera

Nankhumwa adanenetsa kuti pantchitoyi, yomwe ndi ndalama zokwana K198 miliyoni, padayenda chinyengo chachikulu chomwe iye akuti ndi ‘Kashigeti’ ndipo wati ofufuza akamaliza, onse okhudzidwa adzayankha mlandu wosakaza ndalama za boma.

“Polojekiti yaikulu ngati imeneyi idayamba bwanji popanda pulani iliyonse? Chimenechi ndiye chinyengo choyambirira. Chachiwiri, zidatheka bwanji kumusiya kontilakitala kuyamba kumanga mpaka kufika pokhoma malata osazindikira kuti akupanga chinyengo?” adatero Nankhumwa akuthambitsa akuluakulu a khonsolo ya Lilongwe ndi mafunso Lolemba lapitali.

Panthawiyi ndunayi idakayendera chipatalachi itamva kuti chagwa mbali imodzi ndipo mkati monse ndi ming’alu yokhayokha komanso zitseko ndi zimbudzi zidaphotchokaphotchoka ngakhale kuti chipatalacho sichidathe.

Iye adati unduna wake sulekera pomwepa koma ufufuza momwe kontilakitalayo adapatsidwira ntchitoyo ndi zonse zomwe zakhala zikuchitika pachipatalapo ndipo pakapezeka zachinyengo chilichonse, onse okhudzidwa adzazengedwa mlandu.

“Tikukamba apazi ndi ndalama zambiri zedi ndipo nzodabwitsa kuti nthawi yonseyi kontilakitala amagwira ntchito yosaoneka bwino ngati iyi akhonsolo adali kuti? Ichi n’chinyengo chachikulu ndipo tifufuza mpaka ena azengedwapo mlandu apa,” adatero Nankhumwa.

Ndalama zomangira chipatalachi zidachokera kudziko la Japan ndipo Nankhumwa adati ndi momwe zakhaliramu, boma silikudziwa koti lingatenge ndalama zokonzeranso chipatalachi kuti chilongosoke.

Mkulu wa khonsolo ya Lilongwe, Moza Zeleza, adavomereza kuti ntchito yomanga chipatalayo sidayendedi bwino ndipo kuti kontilakitala sadagwire nthawi yomwe amayenera kumaliza ntchitoyo.

Iye adavomereza kuti ntchitoyo idagwiridwa mwa mgwazo, kontilakitala adagwiritsa ntchito zipangizo zosayenera, adaphonya nthawi komanso khonsolo idalephera pantchito yoyang’anira kumangidwa kwa

chipatalacho.

“Ntchitoyi sidayendedi bwino, ayi, moti tidakamang’ala kale kubungwe la a zomangamanga la Malawi Institute of Engineers (MIE) omwe adatipatsa chilolezo cholemba katswiri woti aunike bwinobwino chipatalachi ndi kutiuza choyenera kuchita,” adatero Zeleza.

Iye adati khonsoloyi singachitire mwina koma kudikira zomwe adzanene katswiriyo ngakhale kugwetsa chipatala chonsecho n’kuyambiranso chifukwa momwe chilili, n’chiwopsezo chachikulu kumiyoyo ya anthu.

Zeleza adati chipatalachi chikadayenda bwino nkutha, chikadachepetsa chiwerengero cha amayi a m’madera asanu ndi awiri (7) omwe amayenda mtunda akafuna thandizo la chipatala.

Ena mwa madera omwe akadapindula nawo chipatalachi chikadatha ndi Biwiyo, Area 36, Area 24, Area 22, Chipasula ndi Kaliyeka, madera omwenso kumachokera anthu ambiri mumzindawu.

“Kupatula chipatala cha Kawale, chipatala china chomwe anthu a m’madera asanu ndi awiriwa amadalira ndi cha Bwaila ndipo nchokhacho chomwe amayi oyembekezera a m’maderawa amakachilirako. Chiptala chomwe tikukamba panochi [Biwi], chidakakhalanso ndi malo ochilirako amayi, kutanthauza kuti mavuto ena monga othithikana ku Bwaila akadachepa,” adatero Zeleza.

Mneneri wa unduna wa maboma ang’onoang’ono Muhlabase Mughogho adati undunawu utakayendera chipatalachi koyamba chaka chatha udapeza kuti pansi ndi makoma mudali ming’alu yochititsa mantha.

Iye adati atatsina khutu akhonsolo, adapitako ndipo adakapeza ogwira ntchitoyo akutchinga ming’aluyo ndi matayilosi komabe sizidathandize chifukwa matayilosi ena amapotoka pomata.

Pomwe nduna idakayendera chipatalachi Lolemba lapitali, zitseko zambiri zidali zitaphotchoka, matayilosi ena atamatuka ndipo mpanda usadayambe n’kumangidwa komwe polingalira kuti chipatalachi chili pafupi ndi malo omwera mowa.n

Related Articles

Back to top button