Nkhani

Chipembedzo chikukolezera kupemphapempha m’misewu

Listen to this article

Kukhulupirira chipembedzo kukukolezera mchitidwe wopemphapempha m’misewu, zimene zachititsa kuti ntchito yochotsa opemphawa ivute, watero mkulu wa bungwe limene limachotsa ana m’misewu la Chisomo Children’s Club.

Ngakhale boma lakhala likulengeza kuti aliyense wopezeka akupemphetsa m’misewu adzamangidwa, izi sizikutheka. Sabata zingapo zapitazo, bomalo limalengeza mozungulira mzinda wa Blantyre kuti aliyense wopezeka akupereka ndalama kwa opemphetsa adzamangidwa.

Akuti mawu a Mulungu amavomereza kupereka kwa opempha

Koma mkulu wa bungweli Auspicious Ndamuwa wati ganizo lochotsa opemphetsa m’misewu silingakwaniritsidwe chifukwa zipembedzo zambiri zimalimbikitsa kupereka. Iye adati chikhulupiriro chopereka chidayala nthenje pakati pa Akhristu ndi Asilamu.

“Opemphetsawo amadziwa kuti akapita m’misewu, akakumana ndi anthu opemphera ndiponso a chisoni omwe akawapatse ndalama. Ana ena tikawatenga timawapatsa zofunikira pamoyo wawo, koma ena okonda ndalama ndi kudana ndi sukulu amathawa n’kubwerera m’misewu. Akanakhala kuti anthu sapereka ndalama, vutoli bwenzi litatha,” adatero Ndamuwa.

Akhristu akuganiziridwa kukolezera mchitidwewu pofuna kukwaniritsa mawu a pa Machitidwe a Atumwi 20:35 omwe akuti: “M’zinthu zonse ndakuonetsani kuti mwakugwira ntchito molimbika chomwechi, muthandize ofookawo, ndipo muzikumbukira mawu a Ambuye Yesu. Pajatu iye anati, ‘Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira’.”

Ndamuwa adati Asilamu akutichita izi chifukwa cha Zakati yomwe ndi imodzi mwa ngodya za chipembedzo chawo yomwe achuma amatenga phindu lomwe apeza ndi kugawirako osowa.

Koma mlembi wa Blantyre City Presbytery yomwe ndi gawo la Sinodi ya Blantyre m’busa Baxton Maulidi adati mpingo umathandiza osowa osati kulimbikitsa mchitidwewu chifukwa nthawi ya Yesu opemphetsa adaliponso.

Iye adati vuto ndi kusathandiza anthuwa mokwanira powapatsa njira zoyenera za kapezedwe ka chuma.

“Kulumala, ulesi ndi umphawi zimachititsa anthu kupita pamsewu. Koma palinso olumala ochuluka omwe akugwira ntchito ndi kumathandiza alungalunga.

“Akhristu sangasiye kuthandiza ena. Chofunika ndi kupeza njira zokhazikika zoti azidalira osati kupempha. Munthu wopemphetsa yemwe Petulo m’Baibulo adamuchiritsa sadabwerere pamsewu chifukwa adamuthandiza moyenera,” adatero Maulidi.

Ndipo Sheik Alli Makalani wa pa mzikiti wa pa Mangochi pa boma adati Zakati siyikukhudzana ndi anthu opemphetsa chifukwa Chisilamu chimalimbikitsa kugwira ntchito komanso kholo kusamalira ana ake.

“Wololedwa kupempha ndi mwana wamasiye yemwe alibe womuthandiza ndi wolumala woti sangagwire ntchito. Koma thandizo lake siliyenera kupempha kumsewu. Amatengedwa ndi kukasamalilidwa kumalo oyenera. Sitikondwera ndi opemphetsa mwadala,” iye adatero.

Maulidi ndi Makalani adapempha mabungwe, azipembedzo ndi boma kuti apeze njira zokhazikika zothandiza osowa.

Mneneri wa nthambi ya zosamalira anthu Lucy Bandazi adagwirizana ndi pempholo, koma adati ambiri kupemphetsa ndi khalidwe chabe chifukwa adapindula mundondomeko za boma zowathandiza kuima paokha.

“Pali njira ya mthandizi, feteleza wotsika mtengo ndi zina m’matumba a chitukuko. Undunawu umapereka ukadaulo wa ntchito za manja kwa omwe ali ndi ulumali kudzera ku Malawi Council for the Handicapped (Macoha) ndi Mulanje School for the Blind komwe amaphunzira kusoka, kuluka, ukalipentala ndi ulimi. Akamaliza amapatsidwa zipangizo zoyambira moti ambiri akupemphetsa m’misewu adapindula mu ndondomekozi,” iye adatero.

Bandazi adati aliyense opereka ndalama kwa opemphetsawa akuthandizira kuphwanya lamulo.

“Mavuto omwe amawapititsa m’misewu sangathe ndi kupemphetsa. Ndondomeko za boma ndi zofuna kuti apeze zochita zokhazikika zomwe zipaso zake sizingaoneke nthawi yochepa. Ndi udindo wa aliyense kuonetsetsa kuti anthu osowa akukhala umoyo wabwino, osati mm’sewu,” adatero Bandazi.

Related Articles

Back to top button
Translate »