Nkhani

Chipwirikiti pa Malawi

Listen to this article

Zomwe zikuchitika m’dziko la Malawi zaimitsa mitu ya anthu kuphatikizapo akadaulo pa nkhani zosiyanasiyana.

M’sabata yomwe ikuthayi, zionetsero zomwe zidaima kwa masiku 14 zidayambiranso Lachitatu ndipo tsiku lomwelo, mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika yemwe akuyenera kumva nkhawa za Amalawi ochita zionetserozo adanyamuka ulendo wa ku msonkhano waukulu wa mgwirizano wa maiko ku America.

Ena mwa ochita zionetsero kusonyeza mkwiyo wawo

Kuchokera pomwe zionetserozo zidayamba zotsatira za chisankho cha pa 21 May chitangochitika, Mutharika wakhala akutuma wachiwiri wake Everton Chimulirenji kukamuyimilira m’misonkhano yosiyanasiyana kunja kwa dziko lino. Mutharika adangotuluka sabata yatha kukakhala nawo kumaliro a mtsogoleri wakale wa dziko la Zimbabwe Robert Mugabe.

Malinga ndi kadaulo pandale Makhumbo Munthali, ulendowu ukungotsimikiza kuti Mutharika sakukhudzidwa ngati mtsogoleri ndi zomwe zikuchitika m’dziko lake.

Ena mwa ochita zionetsero kusonyeza mkwiyo wawo

“Anyamuka bwanji momwe zinthu zililimu? Amayenera kukhalapo n’kuona kuti chichitike n’chiyani n’kuonetsa utsogoleri wake. Apapa zikungoonekeratu kuti za anthu ake sizikumukhudza,” adatero Munthali.

Kadaulo pa ndale George Phiri wati zonse zomwe zikuchitika m’dziko muno ndi nthabwala zokhazokha ndipo Amalawi apatsidwa mafunso omwe sakupeza mayankho ake konse.

“Kunena zoona, Mutharika samayenera kunyamuka ulendo wake akadatuma nthumwi ngati momwe wakhala akupangira mmbuyomo. Apa, ngakhale wapita, sikuti ndiye kuti mavutowa atha ayi, akamabwera adzawapezanso,” adatero.

Izi zili apo, bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC), kupyolera mwa mkulu woyendetsa zisankho Sam Alufandika, lidalengeza kuti lichititsa chisankho chapadera kumwera m’boma la Lilongwe November 5, 2019 ngakhale kuli zionetsero zoti mkulu wa bungwelo achoke. Chisankho sichidachitike m’deralo pa 21 May chifukwa mmodzi mwa opikisana nawo, Agnes Penemulungu adamwalira chisankhocho chili pafupi kuchitika.

“Bungwe la MEC lidzakumana ndi onse okhudzidwa ndi chisankhochi pa 3 October 3 kuti lidzafotokoze ndondomeko yachisankhochi,” adatero Alufandika m’kalata yake.

Koma akuluakulu a Malawi Congress Party (MCP) ndi UTM Party ati sizingalole kuti bungwe la MEC liyendetsenso chisankho china mlandu omwe akukana zotsatira ukadali kukhoti.

Zipanizo zidatengera kukhoti MEC ndi Mutharika powaganizira kuti adazondotsa zotsatira za chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino pomwe MEC idalengeza kuti Mutharika ndiye adapambana.

Mlembi wamkulu wa MCP Eissenhower Mkaka adati chipanicho chilibe chikhulupiliro mwa bungwelo chifukwa ungwiro wake ukuyesedwa m’bwalo la milandu.

“MEC siyikuyenera kuyendetsa chosankho chilichonse pokhapokha bwalo la milandu litapeza kuti ndi langwiro ndipo lidayendetsa bwino chisankho chapitacho,” adatero Mkaka.

Mneneri wa UTM Party Joseph Chidanti Malunga adati chisankho chapaderacho chayikidwa nthawi yolakwika.

“Ayi, ndi nthawi yakeyi sizidakhale bwino. A MEC amayenera kudikira asadapangitse chisankho china. Nthawi ndi zochitika sizikugwirizana,” adatero Malunga.

Munthali adadzudzula ganizo la MEC lochititsa chisankho chapadera pomwe Amalawi amachita zionetsero zotsutsana nalo.

“Apa zawonetseratu kuti kwa iwo, palibe kuthekera koti n’kukambirana ndi Amalawi chifukwa asonyeza kuderera konse ndipo atenga Amalawi ngati opanda ntchito,” watero Munthali.

Koma poyankhapo, mneneri wa chipani cha DPP Nicholas Dausi adati MEC ikulondola pa zomwe ikupanga chifukwa ikutsatira malamulo.

“MEC ikuyenera kugwira ntchito yake potsatira gawo 76 ya malamulo imayipatsira mphamvu. Osasokoneza ntchito za MEC chifukwa cha mangawa,” adatero Dausi.

Related Articles

Back to top button