Nkhani

Chisale watuluka n’kumangidwanso

Mawu a wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Saulos Klaus Chilima, womwe amauza anthu m’misonkhano yake ya kampeni kuti adzakwizinga aliyense yemwe adaphwanya malamulo a dziko lino Tonse Alliance ikadzalowa m’boma apherezera.

Amalawi agwira mawu a mtsogoleriyu kaamba koti m’sabata ziwiri zomwe boma la Tonse Alliance lakhala m’boma anthu oposa 20 amangidwa ndipo akuyankha milandu yosiyanasiyana.

Watulutsidwa n’kumangidwanso: Chisale

Ambiri mwa anthuwa ndi otsatira chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) zomwe zachititsa mneneri wa chipanichi Nicholas Dausi kulankhula kuti Tonse Alliance ikumanga anthu pa zifukwa za ndale, koma akadaulo andale apempha boma kuti lisamvere zomwe mkuluyu akulankhula koma kuti ligwiritse ntchito malamulo pounika milandu ya anthuwa.

Ena mwa anthu omwe amangidwa ndi wachiwiri kwa mkulu wa Malawi Revenue Authority, Rosa Mbilizi ndi Norman Chisale, mkulu wa gulu lomwe limateteza mtsogoleri wakale wa dziko lino, Peter Mutharika.

Boma likufuna kudziwa gawo lomwe Mbilizi adatenga pa kugulidwa kwa simenti wa ndalama zoposa K3.2 biliyoni yemwe Mutharika adagula kuchokera m’maiko akunja pamene Chisale akumuganizira kuti akukhudzidwa ndi mchitidwe wozembetsa ndalama.

Magisitiliti Violet Chipawo Lachisanu adapereka belo kwa Norman Chisale, koma adamumanganso ola lisadathe pomuganizira kuti adafuna kupha mzimayi pomuombera ku Chimwankhunda mu mzinda wa Blantyre.

Naye mkazi wake Evalista, yemwe adamuthira unyolo sabata yatha, adali ku ndende ya Dedza.

Evalista, yemwe ndi m’modzi mwa akuluakulu apolisi ku Lilongwe, adamangidwa pamodzi ndi apolisi ena 12 powaganizira kuti akukhudzidwa ndi kuphedwa kwa Buleya Lule.

Lule adaphedwa ali ku polisi atangoyamba kupereka umboni pa mlandu wake wokupha mnyamata wachialubino wa zaka 14 m’boma la Dedza.

Naye wachiwiri kwa mkulu wa bungwe la National Food Reserve Agency (NFRA), Gerald Viola, adamangidwa kaamba kopinyulitsa galimoto ya boma kwa angongole.

Ena otsatira chipani cha DPP omwe avala unyolo ndi khansala wa chipanichi, Jomo Osman, yemwe amadziwika ndi dzina loti Mtopwa 1. Osman adalowa pomuganizira kuti amachitira nkhanza anthu omwe amatsatira zipani zotsutsana ndi DPP.

Dausi adauza atolankhani kuti Tonse Alliance ikumanga otsatira DPP pa zifukwa za ndale.

“Zonsezi ndi ndale chabe osati kuti akumanga anthu omwe adalakwa,” adatero Dausi.

Koma mneneri wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP), Maurice Munthali, adatsutsa zomwe Dausi adalankhula.

“Akumanga anthu ndi apolisi potengera ndi milandu yomwe ali nayo m’kaundula wawo.

“N’kutheka kuti ena mwa omangidwa atha kukhala akuluakulu a zipani zomwe zili mu mgwirizano wa Tonse Alliance,” adatero Munthali.

Iye adati palibe tsiku lomwe akuluakulu a MCP kapena Tonse Alliance adakhala pansi ndi kupanga mndandanda wa anthu woti amangidwe.

Kadaulo wina pa kayendetsedwe ka zinthu m’dziko muno, Vincent Kondowe, adati sakuonapo cholakwika ndi kumangidwa kwa anthuwa.

“Ndi mmene zimayenera kukhalira moti anthuwa akadamangidwa kalekale,” adatero Kondowe yemwe wapempha boma kuti lionetsetse kuti chilungamo chaoneka.

Kadaulo pandale George Thindwa adati kumanga munthu wolakwa sivuto.

“Sikuti anthuwa aloweratu ayi, boma likufuna limve mbali yawo ndi kupeza umboni weniweni kuti chilungamo chioneke,” adatero Thindwa.

Related Articles

Back to top button