Chichewa

Chisamakome mbuzi kugunda galu

Listen to this article

Kawirikawiri tikamva za nkhanza zozungulira chuma cha masiye, timaganizira kuvutidwa kwa amayi ndi ana m’manja mwa abale a mwamuna yemwe wamwalira.
Ichi nchifukwa chakuti nthawi zambiri, mzimayi osiyidwa ndi ana ndi omwe amalandidwa katundu nkumasowa mtengo ogwira akakhala kuti amadalira bambo wopitayo pachilichonse.
Koma polunjika maso pa amayi ndi ana, timaiwala ena mwa anthu amene nthawi zina saganiziridwa pankhani yogawa chuma cha masiye—makolo komanso abale amalemu.
Chimakhumudwitsa kwambiri nchakuti amayi ena amasiye, akakumana ndi abale a mwamuna aulemu, amakhala patsogolo kuphangira zonse kuti zikhale zawo ndi ana, kuponya miyala anthu omwe adachita chilichonse chotheka kuti mwamuna wawo aleredwe bwino.
Osamaiwala kuti ngakhale mwamuna mwaberekerana naye ana, ngakhalenso kupezera chuma china limodzi, mbali ina yamaziko ake ndi makolo ndi abale amene adamulera, nkumuongolera kufikira kukula kuti inu muthe kumukonda.
Mmene inu mumawerengera kuti pali munthu womudalira, momwemonso makolo ndi abale ena amadalira pomwepo.
Inde chuma chamasiye chambiri chiyenera kupita kwa ana, omwe amayenera kuti aphunzire, koma izi sizitanthauza kuti ena omwe amadalira malemuyo aiwalidwe.
Mumati iwowo alowera kuti?
Odalira malemuwatu sakutanthauza omwe amawerengera ndalama zamalemuyo pa chakumwa, ayi. Sindikukambanso za abale ena achibwana osafuna kugwira ntchito nkudziimira paokha.
Ndikukamba za makolo okalamba; anthu ngati abale ang’onoang’ono omwe chifukwa cha umasiye amadalira mchimwene wawo.
Chuma cha masiye si cha mkazi ndi ana okha. Mmene mkazi wamasiye angavutikire wobweretsa chakudya pakhomo akamwalira, ndi momwenso makolo ndi abale a mwamuna amavutikira mbaleyo akatisiya. n

Related Articles

Back to top button
Translate »