Nkhani

Chisankho chapadera chilipolipo lachiwiri

Listen to this article

Mabaloti achisankho chobwereza cha aphungu atatu ndi khansala mmodzi chomwe chiliko Lachiwiri likudzali afika mdziko muno dzulo (Lachisanu) ndipo bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lati ndi lokonzeka kukasiya mabalotiwo mmalo ovotera.

Bungwe la MEC lati zateremu kampeni ikuyenera kutha mawa (Lamulungu) 6 koloko mmawa ndipo lachenjeza kuti opezeka akuchita kampeni nthawiyi itatha adzakumana ndi malamulo oyendetsera chisankho.

Amalawi ena akhala akuvota Lachiwiri likudzali

Mkulu woyang’anira zisankho ku MEC a Harris Potani ati chiletso cha kampenichi chikufikira opikisana nawo pachisankhochi, zipani zawo, owatsatira komanso nyumba zosindikiza ndi kuulutsa nkhani.

“Aliyense akukumbutsidwa kuti ndi kuphwanya lamulo kuchita kampeni nthawi yokhazikitsidwayi itatha. Choncho, ikadzangokwana 6 koloko mmawa wa Lamulungu (mawa) pasadzapezeke opanga kalikonse kosonyeza kukopa anthu ndipo izi zikukhudzanso ofalitsa nkhani,” adatero a Potani.

MEC ichititsa zisankhozi kumpoto cha kummawa kwa boma la Nkhotakota komwe a Martha Chanjo Lunji a DPP adamwalira pa 13 July 2021, pakati cha kummawa kwa boma la Dedza komwe a Mcsteyn Swithin Mkomba a MCP adamwalira pa 27 July 2021, kummawa Mzimba komwe a Wezzie Gondwe omwe adali phungu kumeneko adamwalira pa 1 September 2021.

Chisankho chobwereza cha khansala chichitika kuwodi ya Chimwala ku Balaka komwe khansala Joseph Daniel adamwalira.

Zisankho zapaderazo zinkayenera kukhalako pa 13 August 2021 koma chifukwa nthawiyo mliri wa Covid 19 udavuta kwambiri, bungwe la MEC lidaimitsa zisankhozo n’kudzasankhanso 26 October 2021 ngati tsiku lazisankhozo.

Wapampando wa bungwe la MEC a Chifundo Kachale adalengeza pa 17 September 2021 kuti adaimitsa zisankhozo atakambirana ndi komiti yoona za mliri wa Covid 19 komanso bungwe la Centre for Multiparty Democracy lomwe limaimira zipani zonse zimene zili ndi aphungu ku Nyumba ya Malamulo.

“Titakumana n’kukambirana za momwe mliriwu ulili, tidagwirizana kuti n’kwabwino zisankho ziyambe zaima kaye mpaka kupepuke. Tsiku lina la zisankhozo lilengezedwa mtsogolo muno,” adatero a Kachale.

Iwo adati adzakumana kaye ndi onse okhudzidwa ndi chisankhocho kapena owayimirira kuti adzagwirizane za tsiku lina labwino kuponya votiyo.

Bungwe la MEC layamikira makandideti onse, owatsatira ndi zipani zawo chifukwa chopanga kampeni ya bata ndi mtendere ndipo lati likukhulupilira kuti bata lomwelo lidzaoneka patsiku loponya voti komanso kuwerenga ndi kulengeza zotsatira.

Related Articles

Back to top button