Nkhani

Chisankho chiliko

Listen to this article

Bwalo lalikulu la milandu la Supreme Court dzulo lidagamula kuti bwalo lapadera la Constitutional Court (ConCourt) silidalakwe pogamula kuti chisankho cha pa 21 May 2019 sichidayende bwino.

Choncho, chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino chichitikabe pa 2 July 2020. Ndipo bwalolo lati okhawo amene adalembetsa pa mavoti a 2019 ndiwo adzavotenso, osati amene amalowa m’kaundula watsopano amene wakhala akuchitika.

Nyirenda: Chisankho si chibwana

Lazarus Chakwera yemwe adaimira chipani cha Malawi Congress Party (MCP) ndi Saulos Chilima yemwe adaimira UTM Party adakamang’ala kukhoti kuti bungwe la zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) silidayendetse bwino chisankhocho polengeza kuti mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika ndiye adapambana pachisankhocho.

Pa 3 February chaka chino lidagamula kuti chisankhocho sichidayende bwino ndipo pakhale chisankho china pasanathe masiku 150. Bwalolo lidagamulanso kuti Nyumba ya Malamulo iunike momwe makomishona a MEC adayendetsera chisankhocho. Aphunguwo adapempha Mutharika kuti achotse makomishonawo, limodzi ndi wapampando akuimalimodzi ndi Muluzi yemwe akudziwa bwino za chitukuko.

Polankhula ndi opereka zikalatazo payekhapayekha, wapampando wa MEC Jane Ansah adati pochita kampeni, atsogoleriwo ayenera kubwera ndi njira zatsopano zochitira kampeni. Malinga ndi matenda a Covid-19, boma lidati anthu asakhale oposa 100 malo amodzi, zimene zingakhudze kampeni yomwe idayamba pa 2 May.

Padakalipano, akadaulo a za ndale ena aikapo mlomo pa momwe chisankhochi chikuyendera.

Ndipo kadaulo wina, Humphreys Mvula adachenjeza kuti ngakhale mwayi

iye adakana kuchotsa makomishonawo.wawo Jane Ansah, koma

Koma, m’chigamulo chawo, oweruza 7 a Supreme Court adadabwa chifukwa chomwe MEC ndi Mutharika adachitira apilo alibe mfundo zokwanira.

Mkulu wa oweruzawo, Andrew Nyirenda adati mwa mfundo 137 zimene zidaperekedwa pochita apilo, zidali zokolana, zongobwereza, zosatsata ukadaulo wa zamalamulo komanso zochititsa manyazi.

Nyirenda adati: “Chisankho ndi nsanamira ya demokalase chifukwa kumakhala kusankha atsogoleri. Si zinthu za masewera. Chisankho chiyenera kuyenda mwa chilungamo osati mongawaula kuti pachitika chisankho.”

M’chigamulocho, oweruza adati MEC idaphwanya malamulo a dziko pakayendetsedwe ka chisankhocho.

Iwo anati malamulo a dziko lino samapereka mphamvu kwa aliyense kufuta zotsatira za chisankho. Zidaoneka kuti zotsatira za chisankho zina zidafutidwa ndi utotowa Tippex komanso zikalata za zotsatira zina zidali zochita kukopera zomwe zidali kuphwanya ufulu wa anthu.—Otolera nkhani: STEVE PEMBAMOYO ndi WISDOM CHIROMBO

Related Articles

Back to top button