Nkhani

Chisankho chopanda mudyo?

Listen to this article

Kodi azitaya? Chisankho cha 2019 ena sakuchionetsa dovu pamene zipani 12 zimene zidatulutsa atsogoleri mu 2014, zinayi zokha pakadalipano ndi zimene zaonetsa chidwi chotulutsa atsogoleri.

Izi zikuchitika pamene kwangotsala miyezi 7 yokha kuti dziko lino lichititse chisankho chapatatu chomwe chichitike mu May chaka chikudzachi.

Chibambo: Cheteyu ndiye kuti sitiyimira

Zipani zinayizo ndi Democratic Progressive Party (DPP), Peoples’ Party (PP), Malawi Congress Party (MCP) ndi cha United Democratic Front (UDF). Komanso kuli gulu la United Transformation Movement (UTM) lomwe langobwera kumene limenenso likuonetsa chidwi chodzapikisana nawo.

M’dziko muno muli zipani zoposa 50 zomwe zidalembetsedwa ndipo zina mwa zipanizo sizipikisana nawo pampando wa mtsogoleri wa dziko.

Pocheza ndi Tamvani, zipani zisanu zatsimikiza kuti sizidzapikisananawo mu 2019 malinga ndi kusadabuzika komwe adakuona pachisankho cha 2014.

Mwa zipanizi ndi cha Malawi Forum for Unity and Development (Mafunde), People’s Progressive Movement (PPM), National Salvation Front (Nasaf), United Independence Party (UIP) ndi New Labour Party (NLP).

Chipani cha Pfuko (CCP) chomwe mtsogoleri wake anali Davies Katsonga sichipikisana nawo chifukwa chipanicho chidagawana zida pamene mtsogoleri wake Davis Katsonga adasamuka kukalowa ku DPP.

Mtsogoleri wa Mafunde, George Mnensa adati alibe chilakolako chopikisananawo ngati mtsogoleri wa dziko lino chifukwa chaka chatha kudali atsogoleri 12 zomwe adaziona kuti ndizokwanira ku fuko la Malawi.

“Ndibwino kuti tingothandizira kuti mwina pakhale oimira ochepa zomwe zimapangitsa anthu kuti asankhe molondola,” adatero Mnensa.

Iye adati pali chiyembekezo kuti chipani chake chipanga ubale ndi zipani zina kuti akhale ndi mtsogoleri mmodzi.

Pamene mtsogoleri wa Peoples Transformation Party (Petra), Kamuzu Chibambo adati chete amene waoneka kuchipani kwawo ndi umboni kuti alibe khumbo loimira.

“Achikhala ndikuimira bwezi mutamva zochitika zambirimbiri kuti tiwadziwitse anthu, koma zii amene ndi umboni kuti sitikuyimira. Komanso kugwira ntchito limodzi monga zipani ndi chabwino ku mtundu wa Malawi,” adatero Chibambo.

Kupatula kugwa mochititsa manyazi komwe adakuona mu 2014, zipanizi zidati zinthu zinanso monga kusagwira ntchito kwa lamulo lokhudza zipani (Political Parties Act) lomwe lidavomerezedwa chaka chatha kwathandiziranso.

Iwo akuti sakufuna kudzangodzidzimutsidwa nthawi yothaitha atachititsa kale kampeni.

Kadaulo pa ndale, Ernest Thindwa adati sizodabwitsa kuti zipani zikulakatika pamene tikupita kuchisankho cha 2019 chifukwa cha ndondomeko ya chisankho imene dziko lino limatsatira.

Iye adati m’dziko muno muli ndondomeko yoti amene wapeza mavoti ambiriyo ndi amene wapambana posayang’ana anthu amene sadamuvotere.

“Izi zimapangitsa kuti anthu ambiri agwe mphwayi kuti akapikisane nawo ndiye sizachilendo kumva kuti ena azitaya,” adatero Thindwa.

Iye adati achikhala dziko lino limagwiritsira ntchito ndondomeko ya 50+1, anthu ambiri bwezi ataonetsa chidwi chopikisana nawo.

Related Articles

Back to top button