Chichewa

Chitamponi kanthu pa za fisp

Listen to this article

 

Wapampando wa komiti ya zaulimi m’Nyumba ya Malamulo, Felix Jumbe, wati boma lichitepo kanthu pa za mmene ndondomeko ya Farm Input Subsidy Programme (Fisp) ya zipangizo zaulimi zotsika mtengo ikuyendera polingalira kuti nthawi ikutha.

Jumbe adalankhula izi pocheza ndi Uchikumbe potsatira lipoti la pa 5 January la mmene ntchitoyi ikuyendera lomwe likusonyeza kuti kufika pano, pamatumba 100 alionse a feteleza, 76 okha ndiwo adafika kumalo ogulitsirako zipangizozi.

Ngakhale ena agula kale zipangizo, madera ena sizidafike
Ngakhale ena agula kale zipangizo, madera ena sizidafike

Malingana ndi Jumbe, iyi ndi nkhani yoopsa chifukwa mbewu zimakhala ndi nyengo yake yomwe zimachita bwino zikalandira feteleza ndipo kuti kuthira feteleza nyengoyi itadutsa kale sikungapindule kanthu kwa mlimi.

“Fetelezatu sangothirapo poti wapezeka ayi. Pali nyengo yake malingana ndi mmene mbewu zikukulira chifukwa zikadutsa pena pake, kuthira feteleza kumangokhala kuononga chabe.

“Mwachitsanzo, munthu ungamathire feteleza wokulitsa chimanga chitayamba kale ngaiyaye nkumati ukuchitapo kanthu? Mwezi wa January alimi amayenera zipangizo ali nazo pafupi,” adatero Jumbe.

Nyuzipepala ya The Nation ya pa 8 January idasindikiza kuti zotsatira za mkhumano wa pakati pa nduna ya zamalimidwe, ulimi wamthirira ndi chitukuko cha madzi, Allan Chiyembekeza, ndi eni makampani omwe zikunyamula zipangizozi, adagwirizana kuti ntchitoyi ikuyenera kutha pofika pa 31 December, 2015.

Malingana ndi Jumbe, pomafika pa 5 January ntchitoyi inali ikadali mkati zikusonyeza kuti pena pake pali vuto m’ndondomekoyi ndipo mpofunika kuti akuluakulu omwe akuyendetsa ntchitoyi achitepo kanthu msanga.

Nduna ya zachuma ndi chitukuko, Goodall Gondwe, adauza nyuzipepala yomweyi kuti anthu akupupuluma kufalitsa zolakwika za pulogalamuyi zomwe zikusemphana ndi momwe ikuyendetsedwera chaka chino.

Iye adati n’zomvetsa chisoni kuti zaka zingapo chiyambireni pulogalamuyi, anthu ena amaganizabe kuti idayambitsidwa ndi cholinga chothetsa umphawi pomwe cholinga chake nchakuti anthu azikhala ndi chakudya chokwanira.

“Cholinga cha pulogalamuyi n’chakuti anthu azikolola chakudya chokwanira koma anthu ena amaganiza kuti idabwera kudzathetsa umphawi. Maganizo otere ndiwo amachititsa kuti anthu aziyembekeza kuthandizidwa chaka ndi chaka,” adatero Gongwe.

Malipoti omwe akhala akutuluka chiyambireni pulogalamu ya chaka chinoyi amasonyeza kuti mavuto alipo ambiri omwe gwero lalikulu nkusakhazikika kwa ndalama ya kwacha komwe kudasokoneza kagulidwe ka zipangizo, kukonzetsa makuponi ndi kuyamba kunyamula katunduyu. n

 

 

 

Related Articles

Back to top button