Nkhani

Chitetezo cha mayeso chakhwima

Listen to this article

Mayeso a boma a Sitandade 8, Folomu 2 ndi Folomu 4 a chaka chino aonetsa kusiyana kwa nkhwantha ndi mbatama chifukwa bungwe lolembetsa mayesowo la Malawi National Examinations Board (Maneb) lakhwimitsa chitetezo cha mayesowo.

Malingana ndi mkulu wa bungwe lo a Dorothy Nampota, kupatula kuchulutsa apolisi ndi asikali a nkhondo oteteza mayesowo, bungwelo lakhala likusainitsa makontilakiti onse oyang’anira malo olembera mayeso.

Wapolisi kulondera ana a makalasi awiri

“Sitikusekerera munthu ayi n’chifukwa chake tikufuna kuti onse oyang’anira malo olembetsera mayeso asaine makontilakiti kuti pakapezeka cholakwika chilichonse tidzagwiritse ntchito kontilakitiyo powalanga,” atero a Nampota.

Iwo adatinso aonjezera mgwirizano wa mabungwe oima paokha koma oyang’anira zamaphunziro kuti akhale nawo m’gulu loyendera mmalo molembera mayeso kuti nawo adzakhale ndi lipoti lawo pamapeto.

Mkulu wa mgwirizanowo a Benedicto Kondowe ati kwa nthawi yoyamba Maneb yaonetsa chidwi cholembetsa mayeso ofunadi kusefa pakati pa anzeru ndi opanda nzeru.

“Ateremu atipatsa mphamvu zoti tikhoza kupita paliponse kukaona momwe mayeso akuyendera ndipo izi zithandiza kuti pamapeto, tidzafanizire lipoti la boma ndi lathu. Amalawi ayembekezere mayeso opanda chibwana,” adatero a Kondowe.

Nduna ya zamaphunziro a Agness NyaLonje ati zateremu ophunzira a nzeru akuyenera kulimbikira kuwerenga ndi kukonzekera osati zachibwana kumadalira kuti adzachita chinyengo.

“Tipemphe makolo ndi ana asukulu kuti akhale tcheru, wanzeru akuyenera kulimbikira kuwerenga chifukwa chaka chino kulibe masanje, bungwe la Maneb limodzi ndi unduna wathu takonzeka ndipo sitibwerera mmbuyo,” atero a NyaLonje.

Zonsezi zikutsatira chigumula cha mayeso a Folomu 4 a chaka chatha omwe adalembedwa kawiri chifukwa oyamba adaberedwa mpaka akuluakulu ena a ku bungwe la Maneb adaimitsidwa ntchito.

Kusokonezeka kwa mayesowo kuphatikizapo zovuta zina ngati zokhudza mliri wa Covid-19 zidachititsa kuti mwa ophunzira 138 310 omwe adalemba mayesowo, 57 293 akhoze kuimilira ophunzira 41 mwa ophunzira 100 alionse omwe adalemba mayeso.

Pa za mswahara wa achitetezo komanso aphunzitsi olembetsa mayesowo, a Nampota ati bungwelo liperekeratu mswaharawo kudzera kumaofesi a zamaphunziro a m’maboma.

(a Mpinganjira) ndi wolakwa moti belo yawo ilandidwe apite ku alimandi kundende ya Chichiri mpaka tidzapeleke chilango chawo,” adatero a Degabrielle.lapeza kuti woganiziridwa

Koma woimirira a Mpinganjira pa mlanduwo a Patrice Nkhono adapempha kuti khothi liwaganizire a Mpinganjira popereka chilango chifukwa amagwira ntchito zachifundo, ali ndi banja ali ndi antchito ambiri omwe angavutike iwo akapita ku ndende.

A Nkhono adatinso a Mpinganjira ndi wolakwa koyamba komanso umoyo wawo suli wangwiro kwenikweni kuchokera pomwe adadzapezeka ndi Covid-19 mkatikati mwa mlanduwo.

Koma yemwe amaimira boma a Solicitor General a Reyneck Matemba adati a Mpinganjira akadalingalira za mfundo zonsezi asadapange chiganizo chopalamula mlanduwo.

Iwo adapempha khoti kuti liganizirenso zomwe zikadachitika m’dziko muno a Mpinganjira akadakwaniritsa mapulani awo onyengerera majajiwo ndi ndalama zawo.

“Muganizire kuti pomwe amapalamula mlanduwo mitima ya anthu idali itayaka kale moto moti majaji akadawagonjera a Mpinganjirawa sindikudziwa kuti kukadakhala zotani,” adatero a Matemba.

Iwo adati khoti lipereke chilango chokhwima kuti anthu a ndalama, a mphamvu m’ndale ndi maudindo atengerepo phunziro kuti chuma chawo kapena mphamvu ndi udindo sizingawateteze ku lamulo.

A Mpinganjira amayankha mlandu wa ziphuphu omwe amawaganizira kuti ankafuna kupereka ndalama kwa majaji omwe ankaweruza mlandu wokhudza chisankho cha 2019.

Chisankho cha 2019 chomwe chidakomera chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) malingana ndi bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) pansi pa a Jane Ansah chidapezeka ndi zofooka zambiri.

Mtsogoleri wa chipani cha MCP a Lazarus Chakwera ndi mtsogoleri wa chipani cha UTM Party a Saulos Chilima adakasuma kukhoti kuti chisankhocho sichidayende bwino.

Khoti lidasankha majaji asanu kuti amve n’kuweruza mlanduwo koma ntchito ili mkati majajiwo adadandaula kuti a Mpinganjira amawanyengerera ndi ndalama kuti poweruza akondere a Peter Mutharika a DPP.

Mu April 2021, Degabrielle adati umboni omwe boma lidabweretsa omwe wina ndi omvera pomwe wina ndi owerenga unkatsimikiza kwatunthu kuti a Mpinganjira adayeseradi kuchita katangale.

Iwo adakana milanduyo ndipo boma lidabweretsa mboni zisanu ndi imodzi zomwe zina adali majaji omwe a Mpinganjirawo ankaganiziridwa kuti ankafuna kuwapatsa ziphuphuzo.

A Mpinganjira ndi katakwe pa bizinesi ndipo ndi m’Malawi woyamba kukhala ndi banki yomwe idayamba ngati kampani yobwereketsa ndalama koma pakutha kwa zaka 6 idakula n’kukhala imodzi mwa mabanki 12 omwe ali m’dziko muno.

Banki ya a Mpinganjira yomwe imadziwika kuti FDH Bank idagula masheya 75 mwa masheya 100 alionse a banki yomwe idali yaboma ya Malawi Savings Bank (MSB) ndipo ili ndi nthambi zake m’zigawo zonse komanso m’maboma ena ambiri.

A Mpinganjira ndi katakwe wa zachuma ndipo adachita maphunziro awo omwe adamaliza mu 1984 ku Yunivesite ya Malawi.

Atamaliza maphunzirowo, iwo adagwira ntchito zosiyanasiyana zokhudzana ndi zachuma monga ku kampani yolondoloza ndalama ya Deloitte and Touche, Blantyre Print and Publishing Group, kampani yogulitsa galimoto ya Mandala yomwe pano imadziwika kuti CFAO ndipo amatsogolera nthambi ya zachuma ku kampaniko.

Iwo adagwiranso ntchito ngati zosiyanasiyana mumakampani osiyananso kufikira pomwe iwo adapuma paudindo wawo ngati wapampando wa kampani ya FDH pa 1 September 2020 mlandu wawo utayamba kumene.

Related Articles

Back to top button