Chichewa

Chithunzithunzi cha gogo wathu

Listen to this article

Mukunyasitsa nkhope mwayambana ndi ndani Munthu wokwiya saoneka bwino

Amakhala ngati mtembvo omwe ukanka kumanda Maliro ake ochita kupha ndi mwala

Iyi ndi nyimbo ya Phungu Joseph Nkasa imene inkaphulika malo aja timakonda pa Wenela tsiku limenelo.

Kuchipululu

Kalekalelo, anasankha wolakwika

Waumphawi, ndi umbuli

Anasankha wolakwika

Koma Gervazzio! Sindidziwa kuti amaganiza chiyani posankha nyimbo.

Posakhalitsa idatulukira basi. Adatulukamo Moya Pete, tsinya lili kuno!

“Mumandinena kwambiri, kuti ndinatenga mbuzi 200 kupita kukaonana ndi Bani Kimwezi wa Nations Unie. Nonsense! Nonsense! Mulibe nzeru nonse, kodi simudziwa ndili nawo ochuluka makobidi? Kafunseni mabanki a ku Switzerland! Izi ndi zangazanga ndalama. N’kati ndikuuzeni, pamwezi ndimalandira K1 400 ndiye mukati ndimayenda kuti ndizidya ndalama zanu. Nonsense!” adatero tisanamupatse moni.

Pomwepo, adayamba kukwapula basiyo mokwiya.

“Nonsense kwambiri. Sindidya pakhomo panu. Ndikapita ndi mbuzi 601 dziko lija la Amerigo Vesipusi mwati ndalakwa? Kodi enatu anabwera masauzande!” adazaza Moya Pete.

Inetu ndimadabwa kuti munthu akangolawa zamchere ndithu amapenga ngati mbuzi! Abiti Patuma amaganizanso chimodzimodzi.

“Akulu, khazikitsani mtima pansi. Sikuti mukamalankhula ndi mkwiyo ndiye kuti mukunena zoona. Ndipo enafe timaona kuti munthu akamakalipa, kutenga aliyense ngati chidzukulu chake, timadziwa kuti pali chimene akubisa. Timakumbukatu za Adona Hilida, Mpando Wamkulu ngakhalenso uyu mwati ndani uyu…. Mfumu Mose,” adatero Abiti Patuma.

Abale anzanga, chiwanda choyenda ndi mapazi ichi.

“Ndakwiya kwambiri. Ndikhozanso kuzisiya kwambiri! Kodi mwaiwala kuti gogo uja naye ankakwera ndege monga enanu muchitira kabaza? Bwanji simunkamutsutsa? Ine ndikangoti ndilaweko kabaza wa ndegeyu mwati mfwemfwemfwe! Nonsense!” adatero Moya Pete, uku akunyamula tambula ya madzi ozizira.

Adamwa. Adanyambitira. Adatafunira ngati m’madzimo mudali nsenga.

Gogo amanenedwa apatu ndi uja adandipeza ndikulima osavala ndili kwathu kwa Kanduku. Inde, gogo yemwe uja adapita uku ndi uko kukanena kuti adandipeza ndili buno bwamuswe!

“Mwaiwalatu china chake akulu. Gogo mukunenayo ulamuliro wake udali wayekhayekha ndipo padalibe omutsutsa. Ifetu tikamakutsutsani timakufunirani zabwino,” adatero Gervazzio.

“Ana osakhwima paliombo. Mwaiwala kale zazikulu zimene ndakuchitirani? Munali yani, anthu oipa mwapanga bwanji?” adafunsa Moya Pete.

Palibe adayankha. Aliyense adafa nalo phwete.

“Tsoka lake, mukakhala kuchipinda kwanuko, kudikira kumwa wamkaka tiyi mumaona ngati zonse zikuyenda. Kodi inuyo a Dizilo Petulo Palibe mudawauza anthu kuti mudzathana ndi zoti tizichita Jump Carefully? Nanga zolipira kundagala mudanenapo? Taipa lero?” adatero Abiti Patuma.

Abale anzanga, palibe icho ndidatolapo.

Anga adali malingaliro a chithunzithunzi cha gogo wankhanza ndi bodza uja! Gwira bango, upita ndi madzi. n

 

Related Articles

Back to top button
Translate »