Nkhani

Chiwerengero cha akaidi chakwera

Listen to this article

Chiwerengero cha akaidi m’ndende za m’dziko muno chikunka chikwera.

Mmodzi wa akulu owona za ndende m’dziko muno, Masauko Wiscot, wati chiwerengero cha akaidi chachoka pa 14 430 chaka chatha n’kufika pa 15 000 chaka chino.

Akaidi akudzadzana kwambiri m’ndende za m’dziko lino

Malingana ndi mkuluyu, ndende za m’dziko muno zimayenera kusunga akaidi apakati pa 5 000 ndi 7 000 okha.

“Akabwerebwere ndiwo akuchititsa kuti chiwerengero cha akaidi chizikwera kwambiri m’ndende za m’dziko muno,” adatero Wiscot.

Akaidi omwe Msangulutso yalankhula nawo adati nthawi yowawa kwambiri m’ndende imakhala yogona.

Iwo adati pogona amachita kusanjana ngati matumba ndi kumapumirana, zomwe anadandaula kuti zimaika miyoyo yawo pachiopsezo chotenga matenda osiyanasiyana.

“Ndili ku ndende ya Maula timasowa chakudya, malo wogona, komanso zofunda,” adatero mmodzi mwa anthu omwe adalawapo ukaidi.

Koma Wiscot adati akuluakulu a ndende mogwirizana ndi azamalamulo akuunikanso malamulo oyendetsera ndende za m’dziko muno ndi cholinga chothana ndi mavuto omwe akaidi amakumana nawo.

“Ndende zathu zidamangidwa kalekale chiwerengero cha anthu m’dziko muno chili chochepa.

“Nawo malamulo athu ndi akalekale. Choncho tiyenera kuwaunika mogwirizana ndi momwe zinthu zasintha m’dziko muno,” adatero mkuluyu.

Pofuna kuchepetsa vuto la kudzadza kwambiri kwa akaidi m’ndende, Wiscot adati boma likumanga zipinda zowonjezera.

“Nkhani zomwe zimatisautsa kwambiri ndi malo wogona, chakudya ndi zaumoyo.

“Pofuna kuthana ndi vuto la chakudya, tikumalima tokha mbewu zosiyanasiyana. Boma lidatikomeranso mtima potipatsa dotolo woti azithandiza akaidi,” iye adatero.

Koma wapampando wa komiti yapadera younika za malamulo oyendetsera ntchito zandende m’dziko muno, Ken Manda, adati njira yapafupi yochepetsera vuto la kudzadzana m’ndende ndi kulimbikitsa ukaidi wa kumudzi.

“Njira yapafupi yochepetsera vuto lakuchulukana m’ndende za m’dziko muno ndi kulimbikitsa ukaidi wakumudzi.

“Anthu omwe apalamula milandu ing’onoing’on akuyenera kugwirira ukaidi wawo kumudzi osati m’ndende.

“Kumanga zipinda zogonamo ndi njira yabwino, koma imatenga nthawi yayitali pamene ukaidi wa kumudzi ndi yapafupi,” adatero Manda.

Mmodzi mwa akuluakulu omenyera ufulu wa anthu m’dziko muno, Timothy Mtambo, adati mkaidi ali ndi ufulu womwe munthu wina aliyense ali nawo.

“Kukhala mkaidi sikutanthauza kuti munthuyo alibe ufulu. Ichi n’chifukwa chake boma limawonetsetsa kuti akaidi akupeza thandizo la chipatala akadwala, akulandira chakudya, maphunziro ndi zina zofunika pamoyo wa munthu,” adatero Mtambo yemwe ndi mkulu wa bungwe la for Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR). n

 

Related Articles

Back to top button
Translate »