Nkhani

Chloroquine sachiza Covid-19

Listen to this article

Akatswiri azaumoyo atsutsa zoti chloroquine amachiza coronavirus.

Akadaulowa amathirirapo ndemanga pa kanema yemwe anthu akugawana pa masamba awo a mchezo yemwe akuonetsa dotolo wina wa ku America, Stella Immanuel, akuuza anthu kuti hydroxy-chloroquine ndi mankhwala a Covid-19, koma akatswiri azaumoyo ati zomwe dotoloyo akufalitsa zilibe umboni.

Immanuel adati wakhala akupereka hydroxy-chloroquine, zinc ndi azithromycin kwa odwala 350 a zaka zosiyanasiyana ndipo onse adachira.

Chloroquine ndi mankhwala omwe akhala akugwiritsidwa ntchito pochiza malungo.

Dr Martin Mwaiponya, dotolo wa ku Malawi koma akugwira ntchito ku UK, adati mmbuyomu akatswiri aku UK ndi Brazil amachita kafukufuku ndi cholinga choti apeze ngati hydroxy-chloroquine angachize Covid-19, koma adapeza umboni woti mankhwalawa alibe mphamvu yochiritsa coronavirus.

“Odwala amene adagonekedwa m’chipatala n’kupatsidwa hydroxy-chloroquine, azithromycin ndi mankhwala ena sadaonetse zizindikiro zosintha kapena kusintha m’masiku 15 omwe adalandira mankhwalawa,” adatero Mwaiponya.

Dotoloyu adati kafukufuku wa ku Brazil adamuimitsa kaamba koti akadaulo adatulukira kuti hydroxy-chloroquine atha kudzetsa mavuto ena a mtima.

Iye adati mpofunika kuchita kafukufuku wakathithi kuti umboni weniweni upezeke pa nkhaniyi.

Mwaiponya adati padakali pano dziko lomwe likuchitabe kafukufuku wa hydroxy-chloroquine ndi France.

Naye dotolo komanso mphunzitsi wa pa sukulu ya madotolo ya College of Medicine, Professor Adamson Muula, adatsutsa zoti hydroxy-chloroquine ndi mankhwala a coronavirus.

“Padakali pano palibe mankhwala wochiritsa coronavirus. Choncho sibwino munthu wachipatala kumafalitsa zoti anthu akuchira akamwa hydroxy-chloroquine.

“Mwina zinthu zitha kusintha mtsogolomu kafukufuku wamphamvu akadzachitika,” adatero Muula.

Nalo bungwe la World Health Organisation (WHO) lakhala likuuza anthu kuti hydroxy-chloroquine si mankhwala a coronavirus.

Nkhani ya Immanuel idawanda kwambiri chifukwa choti mtsogoleri wa dziko la America Donald Trump adaiponya patsamba lake la mchezo.

Trump ndi mtsogoleri wa dziko la Brazil Jair Bolsonaro akhala akufalitsa zoti amamwa hydroxy-chloroquine kuti asadwale chloronavirus.

Related Articles

Back to top button
Translate »